‘Muwalitse Kuunika Kwanu’
1 Pa zamakhalidwe ndi zauzimu dzikoli lili mumdima. Kuunika kwa choonadi kumavumbula “ntchito zosabala kanthu” za mdimazi kuti tipeŵe zopinga zakupha zimenezi. N’chifukwa chake, mtumwi Paulo analimbikitsa Akristu kuti: “Yendani monga ana a kuunika.”—Aef. 5:8, 11.
2 “Chipatso cha kuunika” n’chosiyana kwambiri ndi cha mdima wa dziko. (Aef. 5:9) Kuti tionetse chipatso chimenechi n’kofunika kuti tikhale zitsanzo zapadera pamoyo wachikristu, mtundu wa anthu amene Yesu amayanja. Tiyeneranso kuonetsa mikhalidwe monga kudzipereka ndi mtima wonse, kuona mtima, ndi changu pa choonadi. Chipatso ichi chiyenera kuonekera m’moyo wathu watsiku ndi tsiku ndiponso mu utumiki wathu.
3 Walani pa Mpata Uliwonse: Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu.” (Mat. 5:16) Potsanzira Yesu, timawalitsa kuunika kwa Yehova mwa kulalikira Ufumu wa Mulungu ndi zolinga zake. Timawala monga zounikira pamene tipita m’makomo mwa anthu ndiponso pofalitsa choonadi kuntchito, kusukulu, kwa anansi athu, kapena kulikonse kumene tapeza mpata.—Afil. 2:15.
4 Yesu anati ena adzadana ndi kuunika. (Yoh. 3:20) Chotero sitikhumudwa ambiri akakana kuti “chiwalitsiro cha Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Kristu” chiwawalire. (2 Akor. 4:4) Yehova amaona mitima ya anthu ndipo safuna ochita zosalungama pakati pa anthu ake.
5 Pamene titsatira njira za Yehova ndi kusangalala ndi kuunika kwauzimu, tingaunikire ena. Ngati anthu aona mwa makhalidwe athu kuti tili “nako kuunika kwa moyo,” iwonso angasonkhezeredwe kusintha kukhala owalitsa kuunika.—Yoh. 8:12.
6 Mwa kuwalitsa kuunika kwathu, timatamanda Mlengi wathu ndipo timathandiza anthu oona mtima kum’dziŵa ndi kupeza chiyembekezo cha moyo wosatha. (1 Pet. 2:12) Popeza tili ndi kuunika, tiyeni tikugwiritse ntchito kuunikira ena kuti aone njira yotulukira mu mdima wauzimu ndi kuonetsa ntchito za kuunika.