Kuthandiza Ana Athu Kukhalabe M’choonadi: Mbali Yachisanu—Mwa Kuchitira Zinthu Pamodzi
1 Onse mumpingo ayenera kufunitsitsa kuti ana athu akhalebe m’choonadi. M’mbali yomalizayi ya nkhani yathu ino, tipenda mmene ena mumpingo angathandizire makolo, makamaka a mabanja akuluakulu. Komanso, tipenda kufunika kwa banja kukonzekera pamodzi misonkhano ndi kukambirana lemba la tsiku nthaŵi zonse. Pomaliza, tidzaona udindo wa mwana aliyense.
2 Mmene Mungathandizire: Bwanji ngati mayi ndi bambo si olimba mwauzimu ndipo salabadira chilimbikitso cha akulu chopangitsa phunziro la Baibulo la banja nthaŵi zonse? Ngakhale kuti akulu safuna kulanda ntchito yolera ana, angathandize. Akulu, atumiki otumikira ndi ofalitsa ena oyeneretsedwa mu mpingo angadzipereke kuchititsa maphunziro a Baibulo ameneŵa. Ana onse ayenera kukhala ndi mwayi wophunzira Baibulo nthaŵi zonse, ngakhale ngati makolo awo sawapatsa mpata. Iyi ndi nkhani yofunika akulu kufufuza, makamaka pamaulendo obusa mabanja.
3 Ngati makolo ndi ofooka m’choonadi, akulu angauze wofalitsa kukonzekeretsa mwana ubatizo. Izi zingaphatikizepo kuphunzira zofalitsa zoyambira monga buku la Chidziŵitso ndi bulosha la Mulungu Amafunanji. Mwanayo akayamba kuloŵa mu utumiki, ayenera kulimbikitsidwa kupita patsogolo mpaka kudzipatulira ndi kubatizidwa.
4 Onse mumpingo ayenera kuchita chidwi ndi ana pa Nyumba ya Ufumu. Pamsonkhano uliwonse onetsetsani kuti mwawapatsa moni. Apangitseni kumva kuti ali mbali ya mpingo. Lankhula nawoni za mmene sukulu ikuyendera, utumiki, kapena nkhani zina. Sonyezani chidwi ndi zimene akuchita. Alimbikitseni kupanga choonadi kukhala chawochawo ndiponso kutumikira Yehova. Kuchita nawo kwanu chidwi ndi kuwalimbikitsa mwachikondi kungalimbitse ntchito ya makolo awo yowalera “m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” (Aef. 6:4) Alimbikitseni ntchito ya upainiya kukhala cholinga chawo m’moyo. Komanso, dziperekeni kuyenda ndi ana mu utumiki. M’mabanja akuluakulu sikungatheke bambo ndi mayi kutenga ana onse mu utumiki nthaŵi imodzi. Dziperekeni mosangalala kuyenda nawo kotero kuti anawo asamadzione kukhala osafunikira kapena mtolo.
5 Kukonzekera Misonkhano pa Banja: Ndi bwinonso kuti mabanja nthaŵi zonse azikonzekera misonkhano pamodzi kuwonjezera pa phunziro la Baibulo labanja. Makolo angakhale pansi ndi ana awo kukonzekera Nsanja ya Olonda asanakaiphunzire ku mpingo. Thandizani onse kukonzekera mayankho ndipo alimbikitseni kuyankha pamsonkhano. Konzekerani Phunziro la Buku la Mpingo. Ndi bwino kuŵerengera pamodzi Baibulo kaamba ka Sukulu ya Utumiki Wateokalase, ndiponso nkhani zonse za mu sukulu ndi Msonkhano wa Utumiki. Izi zidzathandiza ana anu kukhala n’zizoloŵezi zabwino za kuphunzira akadzakula. Zidzawathandiza kukhala okonda zauzimu ndiponso kufunitsitsa kutumikira Yehova monga mboni yake. Inde, kudzakulitsa chikhumbo chawo chofuna kukhala wofalitsa Ufumu wachangu.
6 Kukambirana Lemba pa Banja: Chofunikanso ndicho kukambirana lemba la tsiku pa banja. Ngakhale kuti nkhaniyi yanenedwa motsindika, si mabanja onse amene akuchita zimenezi. Kukambirana lemba m’maŵa kumathandiza kuliyamba bwino tsiku mwauzimu; koma ngati simungachite nthaŵi imeneyi kambiranani nthaŵi ina. Bambo akachoka kapena ngati sangapangitse, mayi afunika kupangitsa. Gwiritsani ntchito kukambirana lemba kukonzekeretsa ana anu utumiki ndi kudzipatulira komanso ubatizo m’tsogolo. Kukambirana kwabwino kwa tsiku ndi tsiku kumeneku kungakhudze kwambiri chimene mtima wa ana anu umafuna.
7 Mtima Wanu Monga Mwana: Ngati ndinu mwana amene simunayambe kulalikira, tikukulimbikitsani kuyesetsa kukwaniritsa cholinga chimenechi. Kodi mumafuna kutumikira Yehova n’kudzapeza moyo m’dziko lake latsopano? Auzenitu makolo anu zimenezo. Apempheni akuthandizeni kuti muyenere kukhala wofalitsa. Limbikirani ndipo pitani patsogolo m’choonadi kuti muyenerere. Ndiyeno, mukangoyamba, osachita chibwana ndipo nthaŵi zonse khalani wachangu mu utumiki. Khalani waluso polalikira uthenga wabwino pakhomo, ndipo chikhale cholinga chanu kuchita nawo mitundu yonse ya ulaliki. Bwanji osasankha upainiya kukhala cholinga chanu m’moyo? Ino ndi nthaŵi yosankha kutumikira Yehova.—Mlal. 12:1.
8 Pomaliza, pamene tikuyesetsa mu utumiki wathu wachikristu kufunafuna anjala ya choonadi ndiponso kuchita nawo maphunziro a Baibulo mwa khama, tisanyalanyaze ana m’mabanja athuwo. Ndi udindo wathu wachikristu ‘kudzisungira mbumba yathu ya ife eni.’ (1 Tim. 5:8) Izi zimaphatikizapo zosoŵa zawo zauzimu ndi zakuthupi zomwe. (Mat. 4:4) Ngati makolo achita zimene angathe, komanso mothandizidwa ndi akulu ndi ofalitsa okhwima, angayembekeze Yehova kutsogoza ndi kudalitsa khama lawo. Tili ndi chilimbikitso cha m’Malemba pa Miyambo 22:6 chakuti: “Phunzitsa mwana poyamba njira yake [imene imaphatikizapo kukhala wofalitsa Ufumu]; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.”