Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu March: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Tidzayesetsa kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. April ndi May: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Paulendo wobwereza mukapeza achidwi, aikeni pandandanda ya anthu amene mumakawagaŵira magazini. Gaŵirani buku la Chidziŵitso kapena bulosha la Mulungu Amafunanji, n’cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo a panyumba. June: Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? kapena Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Khalani ndi cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba.
◼ Ofalitsa amene akufuna kuchita upainiya wothandiza mu April ayenera kuyamba kukonzekera pakalipano ndipo apereke mafomu awo mwamsanga. Zimenezi zidzathandiza akulu kupanga makonzedwe ofunikira a utumiki wakumunda ndi kupeza magazini ndi mabuku ena okwanira. Lengezani kumpingo mayina a anthu onse omwe avomerezedwa kuchita upainiya wothandiza.
◼ Chikumbutso chidzachitika Lamlungu, pa April 8, 2001. Patsikuli sikudzakhala misonkhano koma kukumana kokonzekera utumiki wakumunda. Akulu angakonze kudzachita phunziro la Nsanja ya Olonda tsiku lina.
◼ Omwe akusonkhana ndi mpingo ayenera kulembetsa magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, kuphatikizapo makope awoawo, kudzera kumpingo, kaya kulembetsako n’koyamba kapena n’kulembetsanso.
◼ Sosaite siikonzera wofalitsa aliyense payekha oda ya mabuku. Woyang’anira wotsogolera ayenera kukonza chilengezo chimene chiyenera kuperekedwa mwezi uliwonse asanatumize ku Sosaite oda ya mabuku a mpingo ya mwezi ndi mwezi kuti onse ofuna mabuku adziŵitse mbale wosamalira mabuku. Chonde kumbukirani mabuku amene ali paoda yapadera.
◼ Zofalitsa Zatsopano Zimene Zilipo:
Mboni za Yehova—Kodi Iwo Ndani? Kodi Amakhulupirira Chiyani?—Chicheŵa, Chitumbuka