Kodi Mayanjano Achikristu ndi Ofunika Motani?
1 “Mutu umodzi susenza denga.” Mwambi umenewu umangothirira ndemanga zimene Baibulo linanena kuti mayanjano n’chinthu chofunika kwambiri pamoyo wa munthu. (Miy. 18:1) Tingapeze chinthu chofunika kwambirichi kwa abale achikristu. Kodi mayanjano amathandiza m’njira ziti?
2 Mu Utumiki: Phindu lalikulu kwambiri n’lakuti abale athu amatilimbikitsa ndi kutithandiza mu utumiki wothandiza anthu. Yesu ankatumiza ophunzira ake “aŵiriaŵiri” kukalalikira. (Marko 6:7; Luka 10:1) Motero, tikayenda ndi ena mu utumiki wakumunda, timaona kuti mawu a pa Mlaliki 4:9, 10 ndi oona. Tikamachitira pamodzi utumiki, chikhulupiriro cha abale athu, kumvera kwawo ndi chikondi chawo, zimatilimbitsa mtima ndi kuwonjezera changu chathu.
3 Timapindula: Ubale wathu umatilimbikitsa ndiponso kutipatsa chitsogozo chothetsera mavuto ndi kukana ziyeso. Anzathu achikristu angatisonyeze Malemba amene amakamba za mavuto athu. Angatipempherere, monga momwenso timachitira. (2 Akor. 1:11) Ndipo zitsanzo zawo zabwino zimatitsogolera kuchita ntchito zabwino ndipo zimatilimbikitsa.
4 Pamisonkhano: Mapindu a mayanjano achikristu timawapeza ngati tifika pamisonkhano yampingo nthaŵi zonse. (Aheb. 10:24, 25) Pulogalamu pamisonkhano imakhala yodzaza ndi malangizo auzimu, ndipo kupezekapo kwathu kumatithandiza kudziŵana bwino ndi okhulupirira anzathu. Misonkhano imeneyi imatipatsa mpata womva abale ndi alongo athu akunena za chikhulupiriro chawo, kaya ndi ku pulatifomu kapena m’gulu la omvetsera. (Aroma 1:12) Unansi wathu ndi abale umakula ngati ticheza nawo tisanayambe misonkhano ndiponso ikatha. Nthaŵi zoterezi zimatipatsa mpata wouza ena zokumana nazo zathu zolimbikitsa chikhulupiriro. Kucheza momasuka ndi anthu okonda Yehova, Mawu ake, ntchito yake ndi anthu ake kumasintha umunthu wathu kukhala wabwinopo.—Afil. 2:1, 2.
5 Timafunika abale athu achikristu. Popanda iwo, kuyenda m’njira yopapatiza yomuka nayo kumoyo kungakhale kovuta kwambiri. Komabe, chikondi ndi chilimbikitso chawo chingatithandize kupitiriza ulendo wopita kudziko latsopano lolungama la Yehova.—Mat. 7:14.