‘Muzipatulapo Kanthu’
Mu mpingo woyambirira wachikristu, anali ndi zosoŵa zakuthupi zofunika kuzisamalira. Malinga ndi mmene munthu aliyense anali kupezera, analimbikitsidwa kuti ‘azipatulapo kanthu’ kukhala chopereka kuti asamalire zosoŵazo. (1 Akor. 16:1-3, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono) Chifukwa cha kuolowa manja kwawo, onse anasangalala kupereka kwa “Mulungu mwa mayamiko ambiri.”—2 Akor. 9:11, 12.
Lerolino ntchito ya padziko lonse ya anthu a Yehova ikukulirakulira, ndipo ikufuna ndalama zambiri. Ndiye chifukwa chake ifenso tiyenera ‘kupatulapo kanthu’ nthaŵi zonse kuti tithandize pa kusoŵako. (2 Akor. 8:3, 4) Tingapereke chuma m’njira zambiri. (Onani Nsanja ya Olonda ya November 1, 2001, masamba 28-9.) Timaona zimenezi monga mwayi umene umadzetsa chimwemwe chenicheni ndipo m’pake kutero.—Mac. 20:35.