Osangalala Pogwirizana ndi Yehova Komanso Mwana Wake
Mwambo Wofunika Kwambiri Pachaka Udzachitika pa March 28
1 Kukumbukira Mgonero wa Ambuye dzuŵa litaloŵa pa March 28, 2002, kudzasonyeza kuti timasangalala pogwirizana ndi Yehova Mulungu ndiponso Yesu Kristu. Pamwambo wapadera kwambiri umenewu, otsalira a Akristu odzozedwa ‘adzayanjana’ mwapadera ndi oloŵa Ufumu anzawo limodzinso ndi Atate ndi Mwana wake. (1 Yoh. 1:3; Aef. 1:11, 12) “Nkhosa zina” zikwizikwi zidzalingalira mwayi wawo wapadera wogwirizana ndi Yehova ndiponso Mwana wake, pokhala ogwirizana nawo maganizo pogwira ntchito ya Mulungu.—Yoh. 10:16.
2 Kugwira Ntchito Mogwirizana Kwambiri: Yehova ndi Yesu akhala ogwirizana nthaŵi zonse ndipo amasangalala kutero. Anakhala ogwirizana kwambiri kwa zaka zambirimbiri munthu asanalengedwe. (Mika 5:2) Chotero aŵiriŵa anakhala okondana zedi. Monga nzeru yokhala ngati munthu, Mwana woyamba ameneyu asanakhale munthu padziko lapansi anati: “Ndinam’sekeretsa [Yehova] tsiku ndi tsiku, ndi kukondwera pamaso pake nthaŵi zonse.” (Miy. 8:30) Kukhalira pamodzi ndi Gwero la chikondi kwa zaka zosaŵerengeka, kunam’thandiza kwambiri Mwana wa Mulungu.—1 Yoh. 4:8.
3 Yehova poona kufunika koombola mtundu wa anthu, anasankha Mwana wake wobadwa yekha, amene anali kukonda anthu kwambiri, kuti apereke nsembe ya dipo yokhayo imene imatipatsa chiyembekezo. (Miy. 8:31) Monga momwe Yehova ndi Mwana wake alili ogwirizana pa cholinga chimodzi, timagwirizanabe nawo komanso ndi anzathu ndi chikondi cholimba pochita chifuno cha Mulungu mosangalala.
4 Tisonyeze Kuyamikira ndi Mtima Wonse: Tingasonyeze kuti timayamikira ndi mtima wonse chikondi cha Yehova ndi nsembe ya Mwana wake, mwa kupezeka pa Chikumbutso komanso kumvetsera mosamala ndi mwaulemu. Ku Chikumbutso adzaunika chitsanzo cha Yesu cha chikondi, kukhulupirika kwake mpaka imfa popereka dipo, ulamuliro wake monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, ndiponso madalitso amene Ufumu umenewo udzabweretsera anthu. Adzatikumbutsanso kufunika kosonyeza chikhulupiriro nthaŵi zonse, kugwira ntchito mwachangu mogwirizana ndi chifuno cha Yehova monga ‘othandizana m’choonadi.’—3 Yoh. 8; Yak. 2:17.
5 Kuthandiza Ena Kudzakhala Nafe: Bungwe la akulu liyesetse kulimbikitsa Mboni zonse zosagwira ntchito m’gawolo kudzapezeka pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu. (Mat. 18:12, 13) Lembani mayina a anthu amene mukufuna kuwaitana kuti musadzaiŵale anthu ena ndiponso kuti mutsimikize kuti onse mwawaitana pamaso m’pamaso.
6 Kodi pali ena amene mukudziŵa kuti angabwere ku Chikumbutso? Alimbikitseni kuona kufunika kwa mwambowu. Aitaneni mosangalala, ndipo dzawalandireni bwino. Tiyeni tiyesetse kuitanira onse amene timaphunzira nawo Baibulo, anthu ena achidwi, ndiponso achibale ndi anzathu ku mwambo umenewu wofunika kwambiri pachaka. Onse amene amaphunzira “mapambanidwe a chizindikiritso cha Kristu Yesu” angapindule ndi dipo. (Afil. 3:8) Amene amakhulupirira nsembe ya Kristu angakhale ndi chiyembekezo chenicheni chopeza moyo wosatha.—Yoh. 3:16.
7 Musayese kuti Chikumbutso sichingakhudze mtima anthu a mtima wabwino. Zaka ziŵiri zapitazo m’dziko la pachilumba la Papua New Guinea, anthu achidwi 11 popita ku mwambowu anayenda maola 17 panyanja yowinduka m’boti laling’ono. Chifukwa chiyani anachita zimenezo? Iwo akuti: “Tinafuna kukachita Chikumbutso cha Kristu pamodzi ndi olambira Yehova anzathu; choncho sitikanachitira mwina.” Talingalirani changu chimene anthu achidwi ameneŵa anasonyeza ndiponso mmene anasonyezera kuti amayamikira komanso kusangalala pogwirizana ndi Yehova, Mwana wake, ndi abale achikristu.
8 Pemphani anthu achidwi onse kuti muziphunzira nawo Baibulo. Alimbikitseni kupezeka pa misonkhano ya mpingo nthaŵi zonse ndiponso kuti aziuza ena choonadi chimene akuphunzira. Athandizeni ‘kuyenda m’kuunika’ ndi ‘kuchita choonadi’ mwa kugwiritsa ntchito mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo m’miyoyo yawo. (1 Yoh. 1:6, 7) Athandizeni kukhala ndi ubwenzi wolimba ndi Yehova ndiponso kupitiriza kuyamikira mwayi wapadera wochita chifuno chake mogwirizana.
9 Ndi mwayi zedi kugwirizana “mu mzimu umodzi, ndi kugwirira pamodzi ndi moyo umodzi chikhulupiriro cha Uthenga Wabwino.” (Afil. 1:27, 28) Chotero tiyeni tiyembekeze mwachidwi kukasangalala ndi mayanjano abwino pa Chikumbutso pa March 28, ndipo tipitirize kuthokoza Yehova ndi Mwana wake.—Luka 22:19.