Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/02 tsamba 3
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki wathu wa Ufumu—2002
Utumiki wathu wa Ufumu—2002
km 6/02 tsamba 3

Zilengezo

◼ Mabuku ogaŵira mu June: Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? kapena Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Ngati eninyumba ali nazo kale zofalitsa tatchulazi, gaŵirani bulosha loyenera limene mpingo uli nalo. July ndi August: Mungagwiritse ntchito lililonse la mabulosha a masamba 32 aŵa: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha, Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani? Kodi Mungachipeze Motani?, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!, ndi “Taonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano.” Mabulosha a Buku la Anthu Onse, Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi? ndiponso Our Problems—Who Will Help Us Solve Them? mungawagaŵire pamene kuli koyenera kutero. September: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha.

◼ Mu January 2001 mipingo yonse anaitumizira mitokoma ya mafomu a Lipoti la Utumiki Wakumunda (S-4). Koma, tikufuna kukukumbutsani kuti chaka chilichonse sitizitumiza mafomu ameneŵa ku mpingo umene sunaitanitse. Mipingo yonse iziitanitsa mafomuŵa nthaŵi zonse mogwiritsa ntchito Fomu Yofunsira Mabuku (S-14) kuti azikhala ndi mafomu okwanira. Muyenera kukhala ndi mafomu a S-4 okwanira kuti wofalitsa aliyense azikhala nalo kuti alembepo maola pamapeto a mwezi uliwonse.

Komanso, kwapezeka kuti mipingo ina situmiza Fomu Yofunsira Mabuku (S-14) mwezi uliwonse. Chomvetsa chisoni n’chakuti, zikupangitsa mipingo imeneyi kusalandira mokhazikika mabuku a abale ndi a mu utumiki wakumunda. Tikupempha mipingo yonse kuti mwezi uliwonse pofika tsiku loyamba la mwezi, izikhala itatumiza oda yawo ya mabuku. Mwa kuchita zimenezi, mpingo komanso anthu a m’munda wanu adzapindula kwambiri mwauzimu.

◼ Nyimbo zotsatirazi n’zimene tikaimbe ku Misonkhano Yachigawo ya chaka chino yakuti “Olengeza Ufumu Achangu.” Nyimbo: 193, 151, 31, 92, 80, 6, 133, 161, 55, 138, 47, 97, 30, 183, 70, 129, 181, 96. Tonse tikonzekere nyimbozi kuti tikaimbire Yehova zitamando ndi mtima wonse komanso mwachimwemwe.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena