Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu July ndi August: Mungagwiritse ntchito lililonse la mabulosha a masamba 32 aŵa: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha, Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani—Kodi Mungachipeze Motani?, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!, ndiponso “Taonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano.” Mabulosha a Buku la Anthu Onse, ndiponso Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi? mungawagaŵire pamene kuli koyenera kutero. September: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. October: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mukapeza anthu achidwi, gaŵirani bulosha la Mulungu Amafunanji, ndipo yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo.
◼ Kuyambira mlungu wa September 16, 2002, tidzayamba kuphunzira buku la Ulosi wa Yesaya—Muuni wa Anthu Onse 2 pa Phunziro la Buku la Mpingo.
◼ Kuyambira mu September, oyang’anira dera azidzakamba nkhani yamutu wakuti “Tetezani Chizindikiro Chanu cha Chikristu!”