Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/02 tsamba 8
  • Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
  • Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Nkhani Yofanana
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
Onani Zambiri
Utumiki wathu wa Ufumu—2002
km 7/02 tsamba 8

Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini

Nsanja ya Olonda July 15

“Kodi mukuganiza kuti anthu ochimwa amalangidwa m’helo? [Yembekezani ayankhe.] Baibulo limanena momveka bwino chilango cha uchimo. [Ŵerengani Aroma 6:23a.] Ndiyeno, kodi helo ndi malo amoto kumene amazunzirako anthu? Kodi amangotanthauza kutalikirana ndi Mulungu? Magazini iyi ikuyankha mafunso ameneŵa mogwiritsa ntchito Malemba.”

Galamukani! Aug. 8

“Anthu ambiri amaona kutchova njuga ngati maseŵera abwino otayirapo nthaŵi. Ena amaona kuti nthaŵi zambiri kumawonongetsa mabanja ndiponso anthu m’deralo sakhalitsana bwino. Galamukani! iyi ikupenda nkhani ya kutchova njuga malinga ndi zimene kafukufuku wina posachedwapa wasonyeza pankhaniyi. Mukhoza kusangalalanso kuŵerenga zimene mfundo za m’Baibulo zimanena pankhaniyi.” Pomusonyeza chitsanzo, ŵerengani 1 Timoteo 6:10.

Nsanja ya Olonda Aug. 15

“Anthu ambiri amaona kuti sikulakwa kukhulupirira malodza ndi miyambo yake. [Kambiranani mfundo imodzi kapena ziŵiri mu nkhani ya m’bokosi la patsamba 5.] Kodi munayamba mwalingalirapo za amene amachititsa zikhulupiriro zimenezi? [Akayankha, ŵerengani 2 Akorinto 11:14.] Magazini iyi ikukamba zimene Baibulo limanena pankhani ya za malodza.”

Galamukani! Aug. 8

“Anthu ambiri akuda nkhaŵa kwambiri ndi kuchuluka kwa ziwawa ndi uchigaŵenga. Mwina mukuvomereza mawu a Mlaliki 8:9. [Ŵerengani lembali ndipo yembekezani ayankhe.] Galamukani! iyi ikufotokoza zimene tingaphunzire pa zinthu za kale ndiponso momwe kupwetekana kumeneku kuthere posachedwapa.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena