Kubereka Ana Mwanzeru—Udindo Wachikristu—Gawo 3
1 Baibulo limasonyeza bwino kuti kukambirana za kugonana pankhani zoyenera sikochititsa manyazi. Mu Israyeli, anthu a Mulungu anauzidwa kusonkhana pamodzi, kuphatikizapo “ana aang’ono,” kuti amvetsere Chilamulo cha Mose chikuŵerengedwa mofuula. (Deut. 31:10-12; Yos. 8:35) Chilamulocho chinatchula mosapsatira nkhani zingapo za kugonana.
2 Yehova Mulungu analenga mwamuna ndi mkazi okhala ndi chilakolako cha kugonana kuti abereke ana, komanso kuti azisangalala monga anthu okwatirana. Kugonana kwa anthu okwatirana ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. Baibulo limauza amuna okwatira kuti: “Ukondwere ndi mkazi wokula naye. . . . Ukodwe ndi chikondi chake osaleka.” (Miy. 5:18, 19) Pachifukwa chimenechi, sikulakwa anthu okwatirana kugonana popanda cholinga chobereka ana, ngati n’zimene akufuna.
3 Inde, okwatirana ambiri amagwiritsa ntchito njira za kulera kuti asangalale ndi mphatso yochokera kwa Yehova imeneyi, popanda kubereka ana. Popeza kuti Baibulo silinena mwachidunji nkhani za kulera, banja lililonse lizisankha lokha njira za kulera mogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo ndiponso chikumbumtima chawo chophunzitsidwa Baibulo. Kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zimene zingathandize banja lachikristu kusankha mwanzeru?
4 Njira ya kulera imene banja lachikristu lasankha iyenera kukhala yolemekeza kupatulika kwa moyo. (Sal. 36:9) Popeza Baibulo limasonyeza kuti moyo wa munthu umayamba mkazi akaima, Akristu adzapeŵa kugwiritsa ntchito njira za kulera zimene zimachotsa mimba, kapena kupha kamwana kamene kayambako. Kwa Yehova izi n’zofanana ndi kupha.—Sal. 139:16; Yer. 1:5; Eks. 21:22, 23.
5 Komabe, pali njira zina za kulera zimene banja lachikristu lingasankhe kugwiritsa ntchito mogwirizana ndi chikumbumtima chawo. Njira zimenezi zimalepheretsa kutenga mimba. Mwina njira za kulera zotchuka kwambiri ndizo kumwa mapilitsi ndi kugwiritsa ntchito makondomu. Zimenezi zimapezeka m’masitolo amene mwayandikana nawo. M’madera ena, m’zipatala zikuluzikulu ndi zing’onozing’ono amapereka ulere zimenezi.
6 N’zoona kuti, anthu ena a chimasomaso amene si Mboni amagwiritsa ntchito mapilitsi olerera ndiponso makondomu molakwika, pofuna kupeŵa mimba ndiponso matenda opatsirana mwa kugonana. Ndiyeno, ambiri amaona njira zimenezi kuti sizabwino. Komabe, izi sizikutanthauza kuti banja lachikristu mogwirizana ndi chikumbumtima chawo silingasankhe kugwiritsa ntchito bwino njira zimenezi. Ngati azigwiritsa ntchito bwino, njira za kulera zimenezi zingathandize kwambiri kupewa kutenga mimba.
7 Inde, kulingalira za Yehova, kuganizirana, kuganizira ana, ndiponso kuiona bwino nkhani ya kubereka ana, zidzathandiza banja lachikristu kusankha kukula kwa banja lawo ndiponso njira za kulera zimene angagwiritse ntchito malinga ndi chikumbumtima chawo.—Onaninso w99-CN 6/15 mas. 27-28; g96-CN 10/8 mas. 13-14; g93-CN 3/8 mas. 30-31.