Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu September: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha kapena Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? October: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mukapeza anthu achidwi, gaŵirani bulosha la Mulungu Amafunanji, ndipo yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo. November: Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? kapena Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Ngati anthu ali nazo kale zofalitsa zimenezi, mungagaŵire mabuku alionse. December: Munthu Wamkulu Koposa Onse Amene Anakhalako. Ngati palibe mungagaŵire Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo, Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu kapena a Munthu?
◼ Tikukumbutsa akulu kutsatira malangizo a mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 1991 patsamba 21-23, onena za anthu ochotsedwa kapena odzilekanitsa amene akufuna kubwezeretsedwa.
◼ Ofesi ya nthambi siilembera wofalitsa oda ya mabuku amene akuwafuna. Woyang’anira wotsogolera azikonza chilengezo mwezi uliwonse asanatumize ku ofesi ya nthambi oda ya mwezi ndi mwezi ya mpingo kuti onse amene akufuna mabuku alembetse kwa mbale woyang’anira mabuku. Chonde, kumbukirani zofalitsa zimene zili za oda yapadera.
◼ Tikufuna kukumbutsa mipingo yonse imene imakasiya yokha ku ofesi ya nthambi ma S(d)-20 (Fomu Yotumizira Zopereka) kuti azipita nawo Lachiŵiri ndi Lachitatu. Zikomo kwambiri posamalira nkhaniyi.
◼ Nthaŵi zina mipingo ndi ofalitsa ena amaimbidwa milandu yokhudza kulambira kwathu Yehova. Kabuku kakuti Defending and Legally Establishing the Good News kanasindikizidwa mu 1950 kuti kathandize pankhani zimenezi. Ngakhale kuti kabukuka kakhala kakugwira ntchito m’mbuyomu, zimene zili m’menemu sizikugwiranso ntchito. Choncho, ofalitsa ndi mabungwe a akulu asagwiritse ntchito chidziŵitsochi pa milandu.
◼ Nkhani ya onse yapadera ya pa nyengo ya Chikumbutso cha 2003 idzakambidwa Lamlungu, pa April 27. Tidzalengeza mutu wa nkhaniyi ndiponso tidzatumiza autilayini yake. Mipingo imene idzakhale ndi woyang’anira dera, msonkhano wadera, kapena tsiku la msonkhano wapadera mlungu umenewu idzakhale ndi nkhani yapaderayi mlungu wotsatizana ndi mlungu umenewu. Mpingo uliwonse usakhale ndi nkhani yapaderayi pasanafike pa April 27, 2003.