Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/02 tsamba 8
  • Futukulani Chuma Chanu cha Utumiki wa Ufumu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Futukulani Chuma Chanu cha Utumiki wa Ufumu
  • Utumiki wathu wa Ufumu—2002
Utumiki wathu wa Ufumu—2002
km 9/02 tsamba 8

Futukulani Chuma Chanu cha Utumiki wa Ufumu

1 Yesu anayerekezera chiyembekezo cha Ufumu ndi chuma chamtengo wapatali. (Mat. 13:44-46) Kodi ndife ofanana ndi amuna a m’mafanizo a Yesu amene anagulitsa chuma chawo chonse kuti agule kanthu kena kofunika kwambiri? Ngati ndi choncho, tidzaika Ufumu wa Mulungu patsogolo, ngakhale kuti zimenezi zingabweretse zovuta zina ndiponso pangafunike kudzimana.—Mat. 6:19-22.

2 Popeza kuti utumiki wathu wa Ufumu ndi chuma, tizifunitsitsa kuufutukula. Kodi zochita zathu zimasonyeza chiyani? Kodi tikufutukula ntchito yathu ya Ufumu? Tingachite zimenezi mwa kuchita mbali zosiyanasiyana za utumiki, monga ntchito ya kunyumba ndi nyumba, kupanga maulendo obwereza, kuchititsa maphunziro a Baibulo ndi ulaliki wamwamwayi.

3 ‘Kodi Ndingafutukule Bwanji Zochita Zanga?’ Popeza kuti chaka chatsopano chautumiki chayamba, ndi bwino kuti aliyense aone zochita zake n’kuona zimene angachite kuti awonjezere nthaŵi imene amakhala mu utumiki wakumunda. Angadzifunse kuti: ‘Kodi ndingasinthe zochita zanga kotero kuti nthaŵi zina kapena nthaŵi zonse ndizichita upainiya wothandiza? Kodi nditasintha zinthu zina, ndingayambe utumiki wa upainiya wokhazikika?’ Apainiya atsopano amene amaikidwa pa September 1 amayenerera kuloŵa Sukulu Yautumiki Waupainiya chaka chotsatira.

4 Ofalitsa ena aika cholinga chakuti azichita kwambiri ulaliki wamwamwayi. Nthaŵi zambiri ntchito imeneyi imabala zipatso zabwino kwambiri. Ena angaone kuti akufunika kusintha mmene amapangira maulendo obwereza kapena maphunziro a Baibulo atsopano kuti azikhala ogwira mtima.

5 Ngati tipeza kuti utumiki wathu umangokhala wa mbali zochepa zokha, kodi tingatani kuti tiufutukule? Awo amene akwaniritsa bwinobwino zolinga zikuluzikulu akuti choyamba tiyenera kutsimikiza kuika zinthu za Ufumu patsogolo, zivute zitani. (Mat. 6:33) N’kofunika kukhulupirira ndi kudalira kwambiri Yehova. (2 Akor. 4:7) M’pempheni ndi mtima wonse komanso nthaŵi zonse kuti akuthandizeni. (Luka 11:8, 9) Tikhulupirire kuti Yehova adzadalitsa zimene tikuchita n’cholinga chofuna kuwonjezera zimene timachita mu utumiki wake.—1 Yoh. 5:14.

6 Kambiranani ndi abale ndi alongo ena amene afutukula bwinobwino utumiki wawo. Afunseni mmene anagonjetsera zopinga popanda kulefuka. Zimene iwo akumana nazo zingakhaledi zimene zikufunika kuti mukhutire kuti n’zotheka kufutukula utumiki.

7 Pamene muŵerenga nkhani zokhudza utumiki wakumunda mu Nsanja ya Olonda kapena mu Utumiki Wathu wa Ufumu, lingalirani mwapemphero za mmene mungagwiritsire ntchito mfundozo mu utumiki wanu. Chitani chimodzimodzinso pa misonkhano ya mpingo kapena ikuluikulu.

8 Yesu anaona utumiki wake kukhala wofunika kwambiri, moti inali ntchito imene ankaikonda kwambiri. Iye ananena kuti: “Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha Iye amene anandituma Ine.” (Yoh. 4:34) Kodi ndi mmene ifeyo timaonera? Ngati timatero, ndithudi tidzapeza njira zofutukulira ntchito yathu ndi kuuza ena “zabwino” zimene zili mosungira chuma chathu.—Mat. 12:35; Luka 6:45.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena