Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu November: Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? kapena Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Ngati mwininyumba ali nawo kale mabuku ameneŵa, mungagaŵire buku lina lililonse. Ngati mpingo wanu ulibe mabuku alionse m’sitoko, mungafunse mipingo imene mwayandikana nayo ngati ili ndi mabuku ena ambiri. December: Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Ngati palibe, mungagaŵire Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo kapena Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? Ngati mpingo wanu ulibe mabuku ameneŵa, funsani mpingo uliwonse umene mwayandikana nawo ngati uli ndi mabuku ambiri amene mungagwiritse ntchito. January: Mankind’s Search for God kapena Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. February: Yandikirani kwa Yehova.
◼ Woyang’anira wotsogolera kapena wina amene iye wamusankha aŵerengere maakaunti a mpingo pa December 1 kapena mwamsanga pambuyo pa detili. Mukatha kuŵerengerako, lengezani kumpingo mukamaliza kuŵerenga lipoti lotsatira la maakaunti.
◼ Mipingo iyambe kufunsira mabaundi voliyumu a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! a 2002 pa oda yawo yotsatira. Mabaundi voliyumuŵa adzakhalapo m’Chingelezi chokha. Adzaonekera monga “Zoyembekezeredwa” pa mipambo yolongedzera katundu wa mipingo kufikira pamene mabaundi voliyumu adzakhalapo ndi kutumizidwa. Mabaundi voliyumu ndi zinthu za oda yapadera.
◼ Macheke a ntchito yapadziko lonse ndiponso a ku Thumba la Nyumba za Ufumu amene anthu amapereka m’mabokosi a zopereka pa misonkhano ya dera, masiku a msonkhano wapadera, misonkhano yachigawo, pa Nyumba ya Ufumu ya m’dera lawo ndiponso amene anthu amatumiza okha ku ofesi ya nthambi, azilembedwa kuti ndalamazo apatse “Watch Tower.” Adiresi ya ofesi ya nthambi yoyang’anira za chuma ndi Watch Tower Bible and Tract Society, P. O. Box 30749, LILONGWE 3.
◼ Alembi azionetsetsa mafomu a S-1 a mwezi uliwonse asanawatumize ku Sosaite ndipo adziŵe izi:
(1) Polemba maola a apainiya, phatikizani maola onse apainiya pamodzi. Musapeze avareji ya mpainiya aliyense. Mwachitsanzo, ngati muli ndi apainiya okhazikika atatu, phatikizani pamodzi maola awo ndipo lembani chiŵerengero cha maola onsewo pamodzi. Chitani zomwezo ndi maulendo obwereza, maphunziro a Baibulo ndiponso zofalitsa zimene agaŵira.
(2) Musamaŵerengere masabusikiripishoni pokhapokha ngati ali magazini amene amatumizidwa kwa anthu papositi. Magazini amene ofalitsa amakapereka pamanja nthaŵi zonse kwa eninyumba musamawaŵerenge ngati masabusikiripishoni.
(3) Mipingo yambiri imachitira lipoti maphunziro a Baibulo ambiri kuposa maulendo obwereza. Izi n’zosatheka, chifukwa chakuti nthaŵi iliyonse imene tapita kukachititsa phunziro la Baibulo timaŵerenganso ulendo wobwereza. Maulendo obwereza azifananako ndi chiŵerengero cha maphunziro a Baibulo amene achitiridwa lipoti. Koma kaŵirikaŵiri maulendo obwereza azikhala ambiri kuposa maphunziro a Baibulo. Nthaŵi zonse muzichitira lipoti maphunziro a Baibulo onse amene mukuchititsa, ndi abanja omwe.
◼ Tikonze: Mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa September tinanena kuti amene amakasiya okha zopereka za mpingo ku ofesi ya nthambi, anapemphedwa kuti azikasiya zoperekazi Lachiŵiri ndi Lachitatu. Koma timafuna kunena kuti Lachiŵiri ndi Lachinayi, osati Lachitatu.
◼ Zofalitsa Zatsopano Zimene Zilipo:
Watch Tower Publications Index 2001—Chingelezi
◼ Makaseti Avidiyo Atsopano Amene Alipo:
Warning Examples for Our Day-On Videocassette—Chingelezi