Phunzitsani Ena Chinenero Choyera
1 Ngakhale kuti Mboni za Yehova zimachokera mwa ‘mitundu, mafuko, ndi anthu’ ambiri, izo n’zogwirizana. Zilidi ndi ubale wa padziko lonse. (Chiv. 7:9) M’dziko ili logaŵanika, zimenezi n’zodabwitsa. Kodi zikutheka bwanji? Zikutheka chifukwa chakuti izo ‘zasintha n’kuyamba kulankhula chinenero choyera.’—Zef. 3:9, NW.
2 Ubwino Wake: Kodi chinenero choyera chimenechi n’chiyani? Ndicho kumvetsa molondola choonadi chopezeka m’Mawu a Mulungu chokhudza Yehova ndi zolinga zake, makamaka choonadi cha Ufumu wa Mulungu. Malinga ndi ulosi wa Yesu, choonadi chimenechi chikudzera m’njira yooneka ya padziko lapansi, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” ndipo anthu “a manenedwe onse” akuphunzira kulambira koona.—Mat. 24:45; Zek. 8:23.
3 Anthu akamaphunzira chinenero choyera, chimawalimbikitsa kusintha moyo wawo kuti ugwirizane ndi miyezo ya Yehova. Amaphunzira ‘kumangika mu mtima [umodzi ndi maganizo amodzi, NW].’ (1 Akor. 1:10) Zimene Mulungu amawaphunzitsa zimawachititsanso kuti akhale ndi khalidwe labwino ndi kalankhulidwe koyenera, ndipo amalankhula zoona, makamaka pankhani youza ena uthenga wabwino. (Tito 2:7, 8; Aheb. 13:15) Kusintha kodabwitsa kumeneku kumalemekeza Yehova.
4 Mwachitsanzo, mwamuna wina amene anafikiridwa ndi uthenga wabwino anali ndi mafunso ambiri, ndipo onse anayankhidwa pogwiritsira ntchito Baibulo. Atachita chidwi ndi zimene anamvazo, anayamba kuphunzira kaŵiri pamlungu ndi kupezeka pamisonkhano. Anadabwa kwambiri poona mmene anam’landirira ku Nyumba ya Ufumu, popeza ambiri kumeneko anali a fuko losiyana ndi lake. Posakhalitsa, iyeyo ndi mkazi wake anasintha moyo wawo nabatizidwa. Chichokereni nthaŵiyo mwamunayo wathandiza anthu ena pafupifupi 40 kuyamba kutumikira Yehova, kuphatikizapo abale ake ambiri. Ngakhale kuti akudwala, anayamba upainiya posachedwapa.
5 Kuphunzitsa Ena: Zimene zikuchitika m’dzikoli zikupangitsa anthu ambiri oona mtima kuganizanso kaŵiri za zolinga zawo ndi moyo wawo. Mofanana ndi Yesu, tikhale ofunitsitsa kuwathandiza. Chofunika kwambiri kuti tithandize anthu oona mtima kuphunzira chinenero choyera ndi maulendo obwereza atanthauzo ndi maphunziro a Baibulo ogwira mtima.
6 Njira imene yakhala yothandiza kwa anthu otanganidwa ndi yochita phunziro la Baibulo lachidule muli choimirira panyumba pawo. (km-CN 5/02 tsa. 1) Kodi mwaiyesapo? Pokonzekera ulendo wobwereza, sankhani ulaliki mu mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2002 umene ukugwirizana ndi mwininyumbayo. Ambiri a maulaliki ameneŵa anakonzedwa kuti akuloŵetseni m’kukambirana bulosha la Mulungu Amafunanji kapena buku la Chidziŵitso. Yeserani ulalikiwo kuti muthe kulumikiza bwinobwino mawu anu oyamba ndi ndime imodzi imene mukambirane. Sankhani lemba limodzi kapena aŵiri m’ndimemo loti mukaŵerenge ndi kukambirana, ndipo konzani funso limene mudzamalize nalo makambiranowo. Funso limeneli lidzakutsogolerani m’ndime imene mukufuna kudzakambirana ulendo wina.
7 Anthu a Yehova akupeza madalitso ochuluka chifukwa chophunzira chinenero choyera. Choncho tiyeni tichite khama kuthandiza ena kugwirizana nafe ‘kuitanira pa dzina la Yehova’ ndi “kum’tumikira ndi mtima umodzi.”—Zef. 3:9.