Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/03 tsamba 7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
km 2/03 tsamba 7

Zilengezo

◼ Mabuku ogaŵira mu February: Buku latsopano la Yandikirani kwa Yehova. March: Gaŵirani buku la Chidziŵitso. Mudzayesetse kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. April ndi May: Gaŵirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mukamapita ku ulendo wobwereza kwa anthu achidwi, ndiponso amene anapezeka pa Chikumbutso kapena amene amapezeka pa misonkhano ina koma sasonkhana mokhazikika ndi mpingo, yesetsani kugaŵira buku la Chidziŵitso.

◼ Woyang’anira wotsogolera kapena wina amene iye wam’sankha aŵerengere maakaunti a mpingo pa March 1, kapena patangodutsa masiku ochepa kuchoka pa detili. Akatha kuŵerengerako, mukalengeze kumpingo mutamaliza kuŵerenga lipoti lotsatira la maakaunti. Ŵerengani kalata, ngati ilipo, yothokoza zopereka za mpingo zothandiza pa ntchito ya padziko lonse ndiponso zopita ku thumba lililonse la gulu.

◼ Mlembi ndi woyang’anira utumiki apende ntchito ya apainiya okhazikika onse. Ngati pali amene zikuwavuta kukwanitsa maola ofunikawo, akulu ayenera kukonza zowathandiza. Onani zina m’makalata a Sosaite apachaka a S-201.

◼ Mutu wa nkhani ya onse yapadera ya pa nyengo ya Chikumbutso cha 2003 udzakhala wakuti: “Kodi Ola la Chiŵeruzo cha Babulo Lafika?” Onani chilengezo chofanana mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa September 2002.

◼ Chifukwa chakuti kulembetsa sabusikiripishoni kudzera papositi kunatha tsopano, m’pofunika kuti mipingo izipatsa abale maganizi atsopano a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! akangofika. Zimenezi zidzathandiza ofalitsa kuti aŵerenge magazini awo ndi kudziŵa zimene zili m’magaziniwo asanapite mu utumiki wakumunda.

◼ Kuyambira ndi magazini ya March 1, 2003, Nsanja ya Olonda ya Chichewa izitulukanso ya zilembo zazikulu.

◼ Mipingo tsopano ingaitanitse mapositikadi osonyeza nthambi ya Malawi. Mapositikadiwa amakhala m’kamulu, ndipo mulu uliwonse uli ndi makadi asanu ndi atatu osonyeza nthambi yatsopano ndi ntchito zosiyanasiyana zimene zikuchitika m’Malawi muno.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena