Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/03 tsamba 8
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
km 3/03 tsamba 8

Zilengezo

◼ Mabuku ogaŵira mu March: Gwiritsani ntchito buku la Chidziŵitso, ndi cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. April ndi May: Gwiritsani ntchito magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Ofalitsa aziuza eninyumba kuti apereke kangachepe kothandizira ntchito ya padziko lonse ngati akufuna kuthandiza. Mukapeza anthu achidwi, gaŵirani bulosha la Mulungu Amafunanji. Yesetsani kuyambitsa phunziro la Baibulo lapanyumba. June: Gaŵirani buku la Chidziŵitso kapena bulosha la Mulungu Amafunanji. Ngati eninyumba ali nazo kale zofalitsa tatchulazi, gaŵirani bulosha loyenerera limene mpingo uli nalo.

◼ Ofalitsa amene akufuna kuchita upainiya wothandiza mu April ayambe panopa kukonzekera ndipo apereke mwamsanga mafomu awo ofunsirapo upainiya. Zimenezi zidzathandiza akulu kukonza dongosolo la utumiki wa kumunda komanso kupeza magazini ndi mabuku ena okwanira. Lengezani kumpingo mwezi uliwonse mayina a anthu amene avomerezedwa kuchita upainiya wothandiza.

◼ Ofesi ya nthambi silembera wofalitsa oda ya mabuku amene akuwafuna. Woyang’anira wotsogolera azilengeza mwezi uliwonse asanatumize ku nthambi oda ya mwezi ndi mwezi ya mpingo kuti onse amene akufuna mabuku auze mbale woyang’anira za mabuku. Chonde, kumbukirani zofalitsa zimene zili za oda yapadera.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena