Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/03 tsamba 7
  • Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
km 3/03 tsamba 7

Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Okondedwa Abale ndi Alongo:

N’ZOSANGALATSATU kwambiri kukulemberani kalata! Tikukuthokozani chifukwa mukupitiriza kusonyeza chikondi ndi kudzimana. Ulendo unonso tinathera maola opitirira 1,000,000,000 pa ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa, kulimbikitsa anthu kuti ayandikire kwa Yehova. Kodi si ulemu wapadera kukhala antchito anzake a Mulungu wathu wolemekezeka ndi Atate wakumwamba?—1 Akor. 3:9.

Tikayang’ana ntchito imene ili m’tsogolo, tikulimba mtima podziŵa kuti mupitiriza kutengera changu ndi chikhulupiriro cha atumiki a Mulungu, amene Baibulo limawatchula. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo anayesetsa kuchita zonse zotheka kuti akhale wogwira mtima popititsa patsogolo zinthu za Ufumu. Mwachionekere, chinali chaka chake chomaliza ali ku Efeso pamene analemba kalata yake yoyamba ku mpingo wachikristu ku Korinto. Potchulapo za cholinga chimene anali nacho, analemba kuti: “Ndidzakhala ku Efeso kufikira Pentekoste. Pakuti panditsegukira pa khomo lalikulu ndi lochititsa, ndipo oletsana nafe ndi ambiri.”—1 Akor. 16:8, 9.

Paulo anali atakonza zopita ku Makedoniya ndi ku Korinto. Komabe, anazindikira za mpata womwe unalipo kuti agwire ntchito yofunika pokhala kaye kwa kanthaŵi ku Efeso. Paulo anali wokonzeka kusintha; anaona mpata wabwino umene akanaugwiritsa ntchito kupititsa patsogolo zinthu za Ufumu kumene analiko, n’chifukwa chake anasintha zimene anafuna kuchita poyamba. Khomo lalikulu lochitira ntchito linali litamutsegukira, ndipo Paulo anali wokonzeka kugwiritsa ntchito mpata umenewo.

Kuti achite zimenezi panafunika ntchito yaikulu yolalikira uthenga wabwino ndi kulimbikitsa mipingo ku Efeso. Nthaŵi ina pambuyo pake Paulo, polankhula ndi akulu a mpingo mu mzinda umenewo, ananena kuti: “Sindinakubisirani zinthu zopindulira, osazilalikira kwa inu, ndi kukuphunzitsani inu pabwalo ndi m’nyumba m’nyumba, ndi kuchitira umboni Ayuda ndi Ahelene wa kutembenuza mtima kulinga kwa Mulungu, ndi chikhulupiriro cholinga kwa Ambuye wathu Yesu Kristu.”—Mac. 20:20, 21.

Mofananamo, ambiri mwa abale ndi alongo inu, mwagwiritsa ntchito mipata imene yakutsegukirani. M’chaka cha utumiki chapitachi, anthu okwana 798,938 akhala akusintha zina ndi zina pamoyo wawo kuti athe kuchita nawo mtundu wina wa utumiki waupainiya. Ena a inu mwayenda mitunda italiitali kuti mukatumikire ngati amishonale. Mukufalitsa uthenga wabwino mwachangu ndi kulimbikitsa mipingo. Ena a inu mwaphunzira chilankhulo china kuti muthe kuthandiza anthu ochokera mayiko akunja amene mukukhala nawo pafupi. Komanso ena asintha zina ndi zina pamoyo wawo kuti athe kukatumikira kumene kuli gawo losagaŵiridwa kapena kumene kuli kusoŵa. Ena aona kuti khomo lalikulu la ntchito latseguka kusukulu, kuntchito, kapena m’njira zina zochitira umboni wogwira mtima, monga pa telefoni. Zochitika padziko lonse zikusonyeza kuti anthu a Mulungu, achinyamata ndi achikulire omwe, akuyesetsa kufunafuna mipata yophunzitsira anthu kulikonse choonadi, ndipo akuipeza.

Dziŵani kuti Yehova amaona ndipo amasangalala kwambiri ndi khama lanu. Baibulo limati: “Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.” (Aheb. 6:10) Chotero, khalani tcheru pa mipata imene ingakuloleni kupititsa patsogolo kulambira koyera. Ena a inu mungathe kufutukula utumiki wanu. Tonsefe tingayesetse kuti utumiki wathu ukhale wogwira mtima kwambiri.

Pochita ntchito yathu yolalikira timatsutsidwa. Kumbukirani kuti Paulo atalankhula za khomo lalikulu la ntchito limene linali litamutsegukira, analemba kuti: “Oletsana nafe ndi ambiri.” Kwa Paulo, anthu otsutsa amenewo anaphatikizapo Ayuda ndi Akunja, ena anachita kumuukira poyera ndipo ena anakonza chiwembu mobisa.—Mac. 19:24-28; 20:18, 19.

Ndi zimene zikutichitikiranso masiku ano. Pamene tikuyandikira chiwonongeko cha dziko loipali, tikuyembekezera kutsutsidwa kwambiri. Satana ali ndi “udani waukulu” ndipo amene akuwada kwambiri ndi anthu amene akutumikira Mulungu. (Chiv. 12:12) Musaiwale kuti Satana ndiye “mkulu wa dziko lapansi.” Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Mukadakhala a dziko lapansi, dziko lapansi likadakonda zake za lokha; koma popeza simuli a dziko lapansi, koma Ine ndinakusankhani inu mwa dziko lapansi, chifukwa cha ichi likudani inu.”—Yoh. 14:30; 15:19.

Ndife otsimikiza kusalola wina aliyense kufooketsa chikhulupiriro chathu mwa Mulungu kapena kutifooketsa pa ntchito yathu yolalikira. Tikudziŵa kuti anthu amene amatiukira ndi kutikonzera ziwembu adzakhalapobe. Koma ife tipitiriza kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu, tili ndi chikhulupiriro kuti Yesu adzaphwanya Satana ndi khamu lake pa nthaŵi yake yoikika ya Yehova. Otsutsa sanalepheretse mtumwi Paulo, ndipo sangaletsenso atumiki a Yehova masiku ano. Ngakhale kuti Satana ndi wokwiya ndipo dzikoli likutida, mzimu wa Yehova ukugwirabe ntchito mwamphamvu pakati pa anthu Ake. N’zolimbikitsatu kwambiri kudziŵa kuti chiŵerengero chatsopanocha olengeza uthenga wabwino chafika pa 6,304,645!

Tikukupemphererani kuti mupitirize kugwiritsa ntchito mipata imene muli nayo kuti mupititse patsogolo zinthu za Ufumu wa Yehova waulemerero. Dziŵani kuti timakukondani aliyense payekha pamene tikutumikira Mulungu Wam’mwambamwamba, Yehova, “ndi mtima umodzi.”—Zef. 3:9.

Ndife abale anu,

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena