Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/03 tsamba 7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
km 4/03 tsamba 7

Zilengezo

◼ Mabuku ogaŵira mu April ndi May: Gaŵirani makope a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Popanga maulendo obwereza kwa anthu achidwi, amene ena mwa iwo amabwera pa Chikumbutso ndiponso/kapena pa zochitika zina za mpingo koma sasonkhana ndi mpingo, yesetsani kuwagaŵira bulosha la Mulungu Amafunanji. Yesetsani kuyambitsa phunziro la Baibulo lapanyumba. June: Gaŵirani buku la Chidziŵitso kapena bulosha la Mulungu Amafunanji. Ngati eninyumba ali nazo kale zofalitsa zimenezi, gwiritsani ntchito bulosha lina loyenerera limene lilipo pampingopo. July ndi August: Mungagwiritse ntchito lililonse la mabulosha a masamba 32 awa: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha, Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani? Kodi Mungachipeze Motani?, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!, ndiponso “Taonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano.”

◼ Kuyambira mu April, tidzatumiza mabaji a msonkhano wachigawo wa 2003 pamodzi ndi mabuku. Simukufunika kuitanitsa zimenezi. Mabaji adzaikidwa m’mipukutu ya mabaji 10 mpukutu uliwonse, malinga ndi kukula kwa mpingo uliwonse. Ngati mpingo ukufuna mabaji ena, itanitsani pa Fomu Yofunsira Mabuku (S-14). Mungaitanitsire aliyense pampingopo pulasitiki loikamo baji ngati anataya la chaka chatha. Komabe, ofalitsa akulimbikitsidwa kusunga mosamala mapulasitikiwa kuti adzagwiritsirenso ntchito.

◼ N’kofunika kuti ofesi ya nthambi ikhale ndi maadiresi ndi manambala a telefoni atsopano a oyang’anira otsogolera ndi alembi onse ngati asintha m’kaundula wake. Komiti ya Utumiki ya Mpingo iziti zimenezi zikangosintha nthaŵi ina iliyonse, izilemba fomu ya Kusintha Keyala ya Woyang’anira Wotsogolera/Mlembi (S-29) ndi kuitumiza mwamsanga ku ofesi ya nthambi.

◼ Alembi a mipingo azisunga mafomu okwanira a Chofunsirapo Utumiki wa Upainiya Wokhazikika (S-205) ndi Chofunsirapo Utumiki wa Upainiya Wothandiza (S-205b). Angaitanitsire mafomuwa pa Fomu Yofunsira Mabuku (S-14). Sungani mafomu okwanira nthaŵi yosachepera chaka chimodzi. Pendani mafomu onse a anthu amene afunsira upainiya wokhazikika kuti mutsimikizire kuti alembedwa bwino musanawatumize ku ofesi ya nthambi. Ngati wofunsirayo sakukumbukira tsiku limene anabatizidwa, angoyerekeza tsikulo ndiyeno asunge limenelo.

◼ Ngati mukukonza zopita kudziko lina ndipo mukufuna kukapezeka pamisonkhano ya mpingo, msonkhano wadera, kapena msonkhano wachigawo, funsani masiku, nthaŵi, ndi malo a misonkhanoyo ku ofesi ya nthambi imene imayang’anira ntchito m’dziko limene mukupitalo. Maadiresi a maofesi a nthambi ali patsamba lomaliza la buku la Yearbook latsopano.

◼ Vinyo wa pachikumbutso amene amagawidwa m’mipingo mu February ndi mu March waperekedwanso ndi Sosaite pa maziko a chopereka chaufulu. Mipingo imene sinaperekebe chopereka chimenechi ingathe kuphatikiza chopereka cha vinyoyo m’miyezi ikubwerayi pa S-20, pamodzi ndi zopereka zawo zaufulu zimene amapereka nthawi zonse ku Sosaite.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena