Kuyamikira Chifundo cha Mulungu
1 Asanakhale Mkristu, mtumwi Paulo ankadana kwambiri ndi Chikristu ndipo ankachita zinthu zachiwawa zambiri pofuna kuti Chikristucho chisafalikire. Komabe, iye anasonyezedwa chifundo chifukwa ankachita zimenezi mosadziŵa. Yehova anasonyeza chifundo ndipo anam’patsa Paulo ntchito yolalikira. Paulo anaiona ntchito imeneyo kukhala yamtengo wapatali. (Mac. 26:9-18; 1 Tim. 1:12-14) Chifukwa choyamikira chifundo cha Yehova, Paulo anadzipereka pokwaniritsa utumiki wake.—2 Akor. 12:15.
2 Chifukwa cha chifundo cha Mulungu, nafenso tapatsidwa utumiki. (2 Akor. 4:1) Monga mmene anachitira Paulo, tikhoza kusonyeza kuyamikira kwathu chifundo chimene tasonyezedwachi mwakudzipereka pothandiza ena kuti apite patsogolo mwauzimu. Njira imodzi imene tingachitire zimenezi ndiyo kuyambitsa ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo.
3 Kuyambitsa Maphunziro a Baibulo: Njira imodzi imene ingatithandize kuyambitsa maphunziro a Baibulo ndiyo kukhala ndi anthu owagaŵira magazini. Tikamapita mobwerezabwereza kwa anthu amene timawagaŵira magazini, timadziŵa bwino nkhaŵa zawo. M’kupita kwa nthaŵi, mwina m’magazini ina mukhoza kutuluka nkhani imene ingatithandize kuyambitsa phunziro la Baibulo mu bulosha la Mulungu Amafunanji. Pa maulendo otsatira, tingathe kupitiriza kukambirana zimene zili m’bulosha la Mulungu Amafunanji tikamamusiyira magazini mwininyumbayo.
4 M’pofunika Kupemphera ndi Kuchita Khama: Kupemphera komanso kuchita khama kungatithandize kwambiri pa ntchito yathu yolalikira. Mlongo wina amene anali mpainiya anali ndi phunziro la Baibulo limodzi ndipo anapempha Yehova kuti am’dalitse pom’patsa maphunziro ena. Ndipo iye anachita zinthu mogwirizana ndi mapemphero akewo. Anaganizira mofatsa za mmene amachitira utumiki wake ndipo anaona kuti pa maulendo obwereza sanali kufunsa anthu ngati akufuna kuphunzira Baibulo. Anayamba kuchita zimenezi ndipo pasanapite nthaŵi yaitali anapeza maphunziro ena aŵiri.
5 Ndifedi amwayi kwambiri pogwira nawo ntchito yofalitsa “Uthenga Wabwino wa chisomo cha Mulungu”! (Mac. 20:24) Posonyeza kuti timayamikira chifundo cha Mulungu, tiyeni tichite khama pothandiza ena kuti nawonso apindule ndi chifundo cha Yehova.