Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu July ndi August: Gwiritsani ntchito bulosha la Njira ya ku Moyo Wosatha—Kodi Mwaipeza? Mabulosha ameneŵa akatha, mungagwiritse ntchito bulosha lina lililonse. Khalani ndi cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo mukapeza munthu wachidwi. September: Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja kapena Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. October: Gaŵirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Ngati mwapeza munthu wachidwi, gaŵirani bulosha la Mulungu Amafunanji, ndipo yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo.
◼ Kuyambira mu September, oyang’anira madera adzakamba nkhani ya onse ya mutu wakuti “N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuopa Mulungu Woona?”
◼ Misonkhano Yachigawo: Tasintha masiku a Misonkhano Yachigawo ku Thete ndi ku Ntcheu. Misonkhano iŵiri imeneyi idzachitika pa September 5 mpaka 7, 2003 m’malo mwa pa August 8 mpaka 10, 2003 ku Thete ndi pa August 15 mpaka 17, 2003 ku Ntcheu.
◼ Zofalitsa Zatsopano Zimene Zilipo:
Imbirani Yehova Zitamando—Zilembo Zazikulum’Chichewa. (Imeneyi ndi nyimbo yokhala ndi zilembo zazikulu koma yopanda madododo, yoyenera anthu amene saona bwino.)