Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
Nsanja ya Olonda Sept. 15
“Masiku ano, anthu ena amaona kuti chikondi chimene chinalipo pakati pa iwowo ndi munthu amene anakwatirana naye chinatha. Kodi anthu ngati ameneŵa angapeze kuti thandizo? [Yembekezani ayankhe.] Baibulo limatitsimikizira kuti mfundo za Mulungu zingatithandize. [Ŵerengani Yesaya 48:17, 18.] Nsanja ya Olonda iyi ikufotokoza mfundo za m’Baibulo zimene zingalimbitse ukwati.”
Galamukani! Sept. 8
“Ngati inu kapena wina m’banja lanu anazunzidwapo ndi munthu wina, mumadziŵa mmene zimapwetekera. [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ya Galamukani! ikupereka mfundo zothandiza kwa anthu ozunzidwa. Ikufotokozanso malonjezo a Mulungu oti m’tsogolo sikudzakhalanso mavuto a kuzunzidwa.” Ŵerengani Mika 4:4.
Nsanja ya Olonda Oct. 1
“Kodi munayamba mwafunsapo kuti, ‘Ngati Mulungu alidi wachikondi ndi wamphamvu kuposa munthu wina aliyense, n’chifukwa chiyani sathandiza anthu amene akuvutika?’ [Yembekezani ayankhe.] Posachedwapa adzathetsa mavuto onse. [Ŵerengani Yesaya 65:17.] Koma panopa, sikuti Mulungu akungoyang’ana osachitapo kanthu pamene ife tikuvutika, monga mmene magazini iyi ikusonyezera.”
Galamukani! Sept. 8
“Mafashoni amakhudza kwambiri moyo wa anthu ochuluka masiku ano. Ena akuganiza kuti anthu akuika mtima mopitirira muyeso pa zimene amavala ndi mmene amaonekera. Inu mukuganiza bwanji? [Yembekezani ayankhe.] Galamukani! iyi ikupereka maganizo oyenera pankhani ya mafashoni.” Ŵerengani Akolose 3:12.