Nzeru Yochokera Kumwamba ndi Yololera
1 Tili oyamikira kwambiri chifukwa cha mmene Mawu a Mulungu asinthira miyoyo yathu, ndipo tikufuna kuti enanso apeze mapindu amene tili nawo. Ndiponso timadziŵa kuti, kuti anthu akapeze madalitso m’tsogolo, zimadalira kulabadira kwawo choonadi. (Mat. 7:13, 14; Yoh. 12:48) Timafunitsitsa kuti iwo alandire choonadi. Komabe, kufunitsitsa kwathuko limodzi ndi changu chathu ziyenera kutsagana ndi kuzindikira kumeneko kuti tipindule anthu ambiri.
2 Mfundo ya choonadi yachindunji yoonetsa kuti chikhulupiriro chimene munthu amachikonda n’chabodza, ngakhale mutapereka Malemba ambiri oikira umboni, kaŵirikaŵiri imakanidwa. Mwachitsanzo, ngati tingotsutsa zikondwerero zofala ndi kunena kuti n’zachikunja, anthuwo sangasinthe maganizo awo pa zikondwerero zimenezo. Koma kukambirana nawo n’kumene kungawathandize. Kodi kukambiranako kuyenera kuchitika motani?
3 Malemba amatiuza kuti “nzeru yochokera kumwamba . . . ndi yamtendere, yololera.” (Yak. 3:17, NW) Liwu lachigiriki lomasuliridwa kuti ‘kulolera’ limatanthauza “kugonjera.” Mabaibulo ena amati “kuganizirana,” “kufeŵa,” kapena “kuleza mtima.” Onani kuti kulolera akugwirizanitsa ndi kukhala wamtendere. Pa Tito 3:2, NW, “kulolera” akutchula limodzi ndi kufatsa ndipo akusiyanitsa ndi kukhala wandewu. Afilipi 4:5, NW, amatilimbikitsa kuti tidziŵike kukhala anthu “ololera.” Munthu wololera amaganizira moyo wa munthu amene akulankhula naye, komanso maganizo ake. Amakhala wokonzeka kugonjera pamene kukhala kofunikira. Kuchita ndi ena mwa njira imeneyo kumatsegula maganizo ndi mitima yawo moti amalabadira pamene tikambirana nawo za m’Malemba.
4 Poyambira Pake. Wolemba zochitika za m’mbiri, Luka, akusimba kuti pamene mtumwi Paulo anali ku Atesalonika, anagwiritsa ntchito Malemba, “natsimikiza, kuti kunayenera Kristu kumva zowawa, ndi kuuka kwa akufa.” (Mac. 17:2, 3) Dziŵani kuti Paulo anachita zimenezi mu sunagoge wa Ayuda. Amene anali kulankhula nawo anali kukhulupirira Malemba Achihebri. Choncho, kunali koyenera kuyambira pa zinthu zimene anali kuvomereza kale.
5 Pamene Paulo anali kulankhula kwa Agiriki ku Areopagi ku Atene, sanayambe mwa kutchula Malemba. M’malo mwake, anayamba ndi zinthu zimene anthuwo anazidziŵa ndi kuzikhulupirira, ndipo iye anagwiritsa ntchito zomwezo powatengera ku mfundo zokhudza Mlengi ndi zolinga Zake.—Mac. 17:22-31.
6 Masiku ano. Pali anthu ambirimbiri amene Baibulo saliona kukhala lofunika pa moyo wawo. Koma mavuto a padzikoli amakhudza munthu aliyense. Anthu amalakalaka moyo wabwino. Ngati choyamba musonyeza nkhaŵa pa zimene zimawavutitsa, kenako n’kusonyeza mmene Baibulo limafotokozera zinthuzo, njira yokambirana imeneyo ingawalimbikitse kuti amve zimene Baibulo limanena za chifuniro cha Mulungu pa anthu.
7 N’kutheka kuti munthu amene mumaphunzira naye Baibulo makolo ake anam’patsa choloŵa cha kum’phunzitsa chipembedzo ndi miyambo ina. Tsopano munthuyo akuphunzira kuti chipembedzocho ndi miyamboyo n’zosam’kondweretsa Mulungu, ndipo akuzikana ndi kukhulupirira zimene akuphunzira m’Baibulo. Kodi angawafotokozere bwanji makolo ake kuti iye akusiya zimenezo? Makolowo angaone kuti mwana wawoyo pokana choloŵa cha chipembedzo chimene anam’phunzitsa, akukana iwo. Choncho, tingafotokozere wophunzira Baibuloyo kuti ayambe watsimikizira makolo akewo kuti amawakonda ndi kuwalemekeza asanafotokoze zifukwa za m’Baibulo zimene wasankhira kuchita zimenezo. Akatero, ndiye kuti adzasonyeza kuti akuyendera “nzeru yochokera kumwamba” imene ili “yololera.”