Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira m’miyezi ya July ndi August: Mabulosha alionse amene mpingo uli nawo. September: Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. October: Tidzagaŵira Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! mwezi wonse. Malangizo ena adzaperekedwa m’tsogolo muno pofuna kuonetsetsa kuti magazini onse amene mudzalandire agwiritsidwa ntchito. Mukapeza munthu wachidwi, gaŵirani bulosha la Mulungu Amafunanji, ndipo mukabwerereko ndi cholinga chokayambitsa maphunziro a Baibulo a panyumba.
◼ Kuyambira m’mwezi wa September, oyang’anira dera azidzakamba nkhani ya mutu wakuti “Kuyang’ana Kutsogolo ndi Chikhulupiriro Ndiponso Molimba Mtima.”
◼ Polalikira m’gawo losagaŵiridwa kwa aliyense, ofalitsa angagaŵire bulosha la Mulungu Amafunanji kapena buku la Chidziŵitso. Ngati eninyumba alinawo kale mabuku aŵiriŵa, angagaŵire buku lina lililonse. Ofalitsa azitenga mathirakiti amitundu yosiyanasiyana kuti azisiya panyumba zimene sanapezepo anthu kapena kupatsa amene akana kulandira mabuku. Tifunika kuyesetsa kubwerera kwa anthu achidwi, makamaka ngati magawo osagaŵiridwawo ali kufupi ndi mipingo imene ikhoza kufikako mosavuta.
◼ Alembi a mipingo ayenera kukhala ndi mafomu okwanira a Chofunsirapo Utumiki wa Upainiya Wokhazikika (S-205) ndi Chofunsirapo Utumiki wa Upainiya Wothandiza (S-205b). Angaode mafomuwa pogwiritsa ntchito Fomu Yofunsira Mabuku (S-14). Khalani ndi mafomu okwanira chaka chimodzi.
◼ Asanatumize mafomu ofunsira utumiki wa upainiya wokhazikika ku ofesi ya nthambi, mlembi wa mpingo ayenera kuonetsetsa kuti zonse pa mafomuwo n’zolembedwa bwino. Ngati amene akufunsira utumikiwo sakukumbukira deti limene anabatizidwa, angoyerekeza detilo ndi kulisunga. Mlembi ayenera kulemba deti limeneli pa Khadi la Mpingo Lolembapo Ntchito za Wofalitsa.
◼ Ofesi ya nthambi imafunika kukhala ndi maadiresi ndi manambala a telefoni amene akugwira ntchito panopa a oyang’anira otsogolera ndi alembi onse m’kaundula wake. Komiti ya Utumiki ya Mpingo iziti zimenezi zikangosintha nthaŵi ina iliyonse, izilemba fomu ya Kusintha Adiresi ya Woyang’anira Wotsogolera/Mlembi (S-29) ndi kuitumiza mwamsanga ku ofesi ya nthambi. Izi zikuphatikizaponso ngakhale kusintha kwa manambala a telefoni.
◼ Popita ku Msonkhano Wachigawo wakuti “Yendani ndi Mulungu,” mudzakumbukire kuti m’pofunika kulemba notsi zachidule, zimene zidzakuthandizani kuyankha pa kubwereza kwa pakamwa kumene kudzaikidwe m’ndandanda ya Msonkhano wa Utumiki chakumapeto kwa chaka chino.