Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 8/04 tsamba 7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
km 8/04 tsamba 7

Zilengezo

◼ Mabuku ogaŵira mu August: Mabulosha alionse amene mpingo uli nawo. September: Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. October: Gaŵirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Malangizo ena adzaperekedwabe m’tsogolo muno kuonetsetsa kuti magazini onse amene mumalandira agwiritsidwa ntchito. Kwa amene aonetsa chidwi, asonyezeni bulosha la Mulungu Amafunanji, ndi cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo. November: Gaŵirani buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Ngati eni nyumba anena kuti alibe ana, gaŵirani bulosha la Mulungu Amafunanji. Pogaŵira buloshali khalani ndi cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo.

◼ Woyang’anira wotsogolera kapena wina amene iye wam’sankha aŵerengere maakaunti a mpingo pa September 1 kapena patangodutsa masiku ochepa kuchokera pa detili. Akatha kuŵerengerako, mukalengeze kumpingo mutamaliza kuŵerenga lipoti lotsatira la maakaunti.

◼ Mipingo iyambe kuitanitsa Kalendala ya 2005 ya Mboni za Yehova, Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—2005 ndi mabuku a 2005 Yearbook of Jehovah’s Witnesses pa fomu yawo yotsatira yofunsira mabuku. Ma Yearbook adzakhala m’Chingelezi basi. Kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku kadzapezeka m’Chicheŵa, m’Chingelezi, ndi m’Chitumbuka pamene Kalendala idzapezeka m’Chicheŵa ndi m’Chingelezi.

◼ Kuŵerengera mabuku ndi magazini onse amene ali m’sitoko kumene kumachitika pachaka kuchitike pa August 31, 2004 kapena pakangodutsa masiku ochepa kuchokera pa detili. Kuŵerengera kumeneku n’kofanana ndi kuŵerengera mabuku kumene mtumiki wa mabuku amachita mwezi uliwonse, ndipo ziŵerengero zonse zilembedwe pafomu ya Kuŵerengera Mabuku (S-18). Chiŵerengero chonse cha magazini amene alipo mungachipeze kwa mtumiki wa magazini. Mpingo uliwonse udzalandira mafomu atatu a Kuŵerengera Mabuku (S-18). Chonde tumizani pepala loyamba ku ofesi ya nthambi pasanafike pa September 6. Sungani pepala lachiŵiri m’faelo yanu. Pepala lachitatulo mungaligwiritse ntchito ngati powonkhetsera. Mlembi adzayang’anire kuŵerengeraku. Iye ndi woyang’anira wotsogolera adzasaine fomuyi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena