Kalata Yochokera ku Nthambi
Okondedwa Ofalitsa Ufumu:
Talandira lipoti latsopano lonena za kusintha kumene kwachitika ku Likulu la Padziko Lonse la Mboni za Yehova. Monga mukudziŵa, nyumba zimenezi zili malo atatu ku New York State, U.S.A. Malo ameneŵa ali ku mzinda wa Patterson ndi Wallkill ndi New York. Nyumba yosindikizira ku Wallkill aiwonjezera ndipo yayamba kugwiritsidwa ntchito. Makina aŵiri atsopano osindikizira, omwe alionse pa okha okhoza kutulutsa magazini okwanira 90,000 pa ola limodzi aikidwa limodzinso ndi makina ena atsopano otha kupanga zikuto zolimba za mabuku zokwana 120 pa mphindi imodzi. Chifukwa chosamutsa nyumba yosindikizira kupita ku Wallkill, zatheka kuti nyumba ya 360 Furman Street ku Brooklyn aigulitse. Pakali pano, abale ndi otanganidwa kwambiri kukonzetsa nyumba za ku 117 Adams Street kuti madipatimenti amene asamutsidwa ku 360 Furman Street adzakhalemo.
Chifukwa cha kusamutsidwa kwa nyumba yosindikizira, abale ndi alongo pafupifupi 300 achoka ku Brooklyn kupita ku Wallkill. Kuwonjezera pamenepo, antchito odzipereka a pa Beteli pafupifupi 100 amene amasamalira za makompyuta ndi zokonza mapulogalamu apakompyuta a Nthambi ya United States asamuka ku Wallkill kupita ku Brooklyn, kumene tsopano kuzichitikira ntchito yaikulu ya Dipatimenti ya Information Systems. Dipatimenti imeneyi imayang’anira ntchito za makompyuta zimene zimachitika m’maofesi a nthambi apadziko lonse.
Mudzasangalala kumva kuti anthu oposa 185,000 anapezeka pa mwambo wa Chikumbutso cha imfa ya Kristu m’Malawi muno. Apainiya othandiza anakwana 3,449 m’mwezi wa April.
Mofanana ndi inuyo, ifenso tikuyembekeza kukhala ‘ochuluka mu ntchito ya Ambuye’ pamene tikuyamba chaka chatsopano cha utumiki cha 2005.—1 Akor. 15:58.
Ndife abale anu,
Ofesi ya Nthambi ya Malaŵi