Kodi Pangakhale Vuto Lililonse ndi Kuchita za Matsenga ndi Ufiti?—Gawo 1
1. Kodi matsenga n’chiyani?
1 Kuyambira kalekale, munthu wachita chidwi ndiponso kulamulidwa ndi za matsenga. Kale ku Peresiya kunali gulu la ansembe amene anali akatswiri pankhani ya zamatsenga. Matsenga kwenikweni, ndiwo kuyesa kulamulira mphamvu zachilengedwe kapena mphamvu zinazake zomwe si zaumunthu kuti zichite zomwe munthu akufuna.
2. Kodi chikhulupiriro cha matsenga ndi ufiti n’chofala motani?
2 M’zaka za m’ma 1700 B.C.E. ku Igupto kunali ansembe ochita zamatsenga. Matsenga analinso ofunika kwambiri m’chipembedzo cha Akasidi ku Babulo kalelo m’zaka za m’ma 700 B.C.E. (Gen. 41:8, 24; Yes. 47:12-14; Dan. 2:27; 4:7) Khalidwe limeneli linafalikira pakati pa Agiriki ndi Aroma akale. Kenako linafika m’zaka za m’ma 500 mpaka m’zaka zathu zino za m’ma 2000. Amene amakhulupirira matsenga ndi ufiti ndi anthu osaphunzira ndiponso anthu ophunzira kwambiri. Atsogoleri a chipembedzo cha Chisilamu ndi a Matchalitchi Achikristu nawonso amakhulupirira matsenga.
3. Malinga ndi zimene ambiri amakhulupirira, kodi mphamvu ya matsenga imachokera kuti?
3 Malinga ndi zimene ambiri mu Africa muno amakhulupirira, pali mphamvu inayake yauzimu yopambana mphamvu ya anthu. Mulungu ndiye amailamulira. Mizimu ndi makolo angathe kuigwiritsa ntchito mphamvuyo. Ndipo amati anthu ena amadziwanso mmene angaipezere ndi kuigwiritsa ntchito pa zinthu zabwino (kutsirika) kapena kuchita zoipa (kulodza).
4. Kodi kuchita matsenga n’kutani, ndipo anthu amakhulupirira zoti matsenga angachite chiyani?
4 Matsenga amaphatikizapo kulodza, kutemberera, ndi kugwiritsa ntchito diso lankhwezule kuvulazira adani a munthu. Anthu amakhulupirira kuti amatsenga ali ndi mphamvu yotumiza mileme, mbalame, ntchentche, ndi nyama zina kuti zikapweteke anthu anzawo. Ambiri amakhulupirira kuti matsenga amachititsa mikangano, kusabala, matenda, ngakhale imfa.
5. Kodi anthu ambiri amakhulupirira chiyani za mfiti, ndipo anthu ena amene anali mfiti aulula zoti chiyani?
5 Zimenezi sizisiyana ndi ufiti. Anthu amati mfiti zimasiya matupi awo usiku ndi kuuluka kupita kwina, kaya kukakumana ndi mfiti zina kapena kukawononga miyoyo ya adani awo. Popeza matupi a mfiti amakhalabe aligone pabedi, umboni wotsimikiza nkhani zimenezi umaperekedwa makamaka ndi anthu amene anasiya ufiti. Mwachitsanzo, magazini ina ya mu Africa muno ili ndi mawu onenedwa ndi anthu ena amene anali mfiti (makamaka atsikana). Iwo anaulula kuti: “Ndinapha anthu 150 mwa kuchititsa ngozi za galimoto.” “Ndinapha ana asanu mwa kuyamwa magazi awo onse.” “Ndinapha anyamata atatu amene ndinali nawo pachibwenzi chifukwa anathetsa chibwenzi chathu.”
6. Kodi kutsirika n’kutani, ndipo okonda kutsirika amachita zotani?
6 Kutsirika amati kumateteza munthu ku zoipa. Okonda kutsirika amavala mphete kapena makoza amatsenga. Amamwa kapena kudzola m’thupi mankhwala owateteza. M’nyumba zawo amabisa kapena kukumbira pansi zinthu zimene amaganiza kuti zili ndi mphamvu yowateteza. Amakhulupirira njirisi zolembapo mawu a m’Korani kapena a m’Baibulo. Kodi pali vuto lililonse ndi kuchita zamatsenga? Nkhani yotsatira idzafotokoza zimenezi mwatsatanetsatane.