Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu January: Gawirani buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. February: Tidzagawira buku la Yandikirani kwa Yehova. March 1 mpaka 13: Pitirizani kugawira buku la Yandikirani kwa Yehova, March 14 mpaka April 17: Ntchito yapadera yogawira bulosha la Dikirani! Ngati anthu aonetsa chidwi chenicheni asonyezeni buku la Chidziŵitso ndi cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo la panyumba. April 18 mpaka 30 ndi May: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Popanga maulendo obwereza kwa anthu achidwi, kuphatikizapo amene anapezeka pa Chikumbutso kapena pa zochitika zina zauzimu koma sasonkhana ndi mpingo mokhazikika, yesetsani kuwagawira buku la Lambirani Mulungu. Cholinga chathu chikhale choyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba, makamaka ndi anthu amene anaphunzira kale buku la Chidziŵitso ndi bulosha la Mulungu Amafunanji. June: Gawirani buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso, ndipo ngati anthuwo anena kuti alibe ana, gawirani bulosha la Mulungu Amafunanji. Yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba.
◼ Woyang’anira wotsogolera kapena wina amene iye wam’sankha awerengere maakaunti a mpingo pa March 1, kapena patangodutsa masiku ochepa kuchokera pa detili. Akamaliza kuwerengerako, mukalengeze kumpingo powerenga lipoti lotsatira la maakaunti.
◼ Mlembi ndi woyang’anira utumiki apende ntchito ya apainiya onse okhazikika. Ngati pali amene zikuwavuta kukwanitsa maola ofunikawo, akulu ayenera kukonza zowathandiza. Onani mfundo zina m’makalata apachaka a S-201.
◼ Mutu wa nkhani ya onse yapadera ya pa nyengo ya Chikumbutso cha 2005 udzakhala wakuti, “Kodi N’chifukwa Chiyani Yesu Anavutika Ndiponso Kufa?” Onani chilengezo cha nkhani yomweyi mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa September 2004.
◼ Aliyense afunika kuti adzapezeke pa Msonkhano wa Onse, pa Lamlungu, pa March 20, chifukwa padzakhala chilengezo chapadera chokhudza thandizo limene lidzaperekedwa kwa ofalitsa.
◼ Ofesi ya nthambi silembera ofalitsa oda ya mabuku amene akuwafuna. Woyang’anira wotsogolera azikonza chilengezo mwezi uliwonse choti chiziperekedwa asanatumize ku nthambi oda ya mwezi ndi mwezi ya mpingo kuti onse amene akufuna mabuku auze mbale woyang’anira za mabuku. Chonde kumbukirani mabuku amene ali zinthu zofunsira mwapadera.
◼ Ndife osangalala kulengeza kuti buku la Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo tsopano lilinso m’Chitumbuka. Tikulimbikitsa mipingo yonse kutumiza oda yawo ya bukuli potsatira njira yanthawi zonse.