Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/05 tsamba 7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
km 3/05 tsamba 7

Zilengezo

◼ Mabuku ogawira pa March 1 mpaka 13: Pitirizani kugawira buku la Yandikirani kwa Yehova. March 14 mpaka April 17: Ntchito yapadera yogawira bulosha la Dikirani! Ngati anthu aonetsa chidwi chenicheni asonyezeni buku la Chidziŵitso ndi cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo la panyumba. April 18 mpaka 30 ndi May: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Popanga maulendo obwereza kwa anthu achidwi, kuphatikizapo amene anapezeka pa Chikumbutso kapena pa zochitika zina zauzimu koma sasonkhana ndi mpingo mokhazikika, yesetsani kuwagawira buku la Lambirani Mulungu. Cholinga chathu chikhale choyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba, makamaka ndi anthu amene anaphunzira kale buku la Chidziŵitso ndi bulosha la Mulungu Amafunanji. June: Gawirani buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso, ndipo ngati anthuwo anena kuti alibe ana, gawirani bulosha la Mulungu Amafunanji. Yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. July: Gawirani lililonse la mabulosha awa: Buku la Anthu Onse, Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu, Njira ya ku Moyo Wosatha—Kodi Mwaipeza?, ndi Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!

◼ Mipingo ifunika kuti izipereka kwa abale magazini atsopano a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! akangofika. Zimenezi zidzathandiza kuti ofalitsa athe kudziwiratu bwino nkhani zimene zili m’magaziniwo asanapite mu utumiki wa kumunda. Muyeneranso kupereka Utumiki Wathu wa Ufumu kwa ofalitsa ukangofika. Mungaupereke kudzera m’Maphunziro a Buku a Mpingo.

◼ Alembi a mipingo ayenera kukhala ndi mafomu okwanira a Chofunsirapo Utumiki wa Upainiya Wokhazikika (S-205) ndi Chofunsirapo Utumiki wa Upainiya Wothandiza (S-205b). Angaode mafomuwa pogwiritsa ntchito Fomu Yofunsira Mabuku (S-14). Khalani ndi mafomu okwanira chaka chimodzi.

◼ Chikumbutso chidzachitika Lachinayi pa March 24, 2005. Ngati pa tsiku limeneli mpingo wanu umakhala ndi misonkhano, muyenera kuisinthira misonkhanoyo ku tsiku lina la mlungu womwewu ngati Nyumba ya Ufumu sidzakhala ikugwira ntchito. Ngati zimenezi zili zosatheka ndipo zakhudza Msonkhano wa Utumiki, ndiye kuti nkhani zimene mukuziona kuti n’zothandiza mu mpingo wanu mungadzaziphatikize ku Msonkhano wina wa Utumiki.

◼ Zofalitsa Zatsopano Zomwe Zilipo:

Uthenga Wabwino wa Anthu a Mitundu Yonse—Chichewa, Chingelezi, Chitumbuka

Dikirani!—Chichewa, Chingelezi, Chitumbuka

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena