Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/05 tsamba 7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
km 4/05 tsamba 7

Zilengezo

◼ Mabuku ogawira pa March 14 mpaka April 17: Ntchito yapadera yogawira bulosha la Dikirani! Ngati anthu aonetsa chidwi chenicheni asonyezeni buku la Chidziŵitso ndi cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo la panyumba. April 18 mpaka 30 ndi May: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Popanga maulendo obwereza kwa anthu achidwi, kuphatikizapo amene anapezeka pa Chikumbutso kapena pa zochitika zina zauzimu koma sasonkhana ndi mpingo mokhazikika, yesetsani kuwagawira buku la Lambirani Mulungu. Cholinga chathu chikhale choyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba, makamaka ndi anthu amene anaphunzira kale buku la Chidziŵitso ndi bulosha la Mulungu Amafunanji. June: Gawirani buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso, ndipo ngati anthuwo anena kuti alibe ana, gawirani bulosha la Mulungu Amafunanji. Yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. July: Gawirani lililonse la mabulosha awa: Buku la Anthu Onse, Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu, Njira ya ku Moyo Wosatha—Kodi Mwaipeza?, ndi Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!

◼ Kuyambira mu April, tidzatumiza mabaji a msonkhano wachigawo wa 2005 pamodzi ndi mabuku. Simukufunika kuitanitsa mabajiwa pokhapokha ngati mpingo wanu umasamaliranso kagulu kolankhula chinenero chakunja. Malinga ndi kukula kwa mpingo uliwonse, mabaji adzaikidwa m’mipukutu ya mabaji 25 mpukutu uliwonse. Ngati mpingo ukufuna mabaji ena, itanitsani pa Fomu Yofunsira Mabuku (S-14). Ngati pampingopo pali amene akufuna mapulasitiki oikamo baji, mungawaitanitsire.

◼ Ofesi ya nthambi iyenera kukhala ndi maadiresi ndi manambala a telefoni amene akugwira ntchito panopo a oyang’anira otsogolera ndi alembi onse m’kaundula wake. Zimenezi zikangosintha nthawi ina iliyonse, Komiti ya Utumiki ya Mpingo izilemba ndi kusaina fomu ya Kusintha Adiresi ya Woyang’anira Wotsogolera/Mlembi (S-29) ndi kuitumiza mwamsanga ku ofesi ya nthambi. Zimenezi zikuphatikizapo kusintha kulikonse kwa manambala a telefoni.

◼ Alembi a mipingo azisunga mafomu okwanira a Chofunsirapo Utumiki wa Upainiya Wokhazikika (S-205) ndi Chofunsirapo Utumiki wa Upainiya Wothandiza (S-205b). Angaitanitse mafomuwa pa Fomu Yofunsira Mabuku (S-14). Sungani mafomu okwanira pafupifupi chaka chimodzi. Pendani mafomu onse a anthu amene afunsira upainiya wokhazikika kuti mutsimikizire kuti ayankha mafunso onse.

◼ Mipingo iyambe kuitanitsa mavoliyumu a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani a 2004. Mavoliyumuwa adzakhalapo mu Chingelezi basi. Mavoliyumuwa azidzaonekera monga “Zoyembekezeredwa” pa mipambo yolongedzera katundu wa mpingo kufikira pamene adzayambe kupezeka ndi kutumizidwa. Mavoliyumu ndi zinthu zofunsira mwapadera.

◼ Tikufuna kukumbutsa mipingo yonse kuti izitumiza Malipoti a Mpingo a Utumiki wa Kumunda (S-1) ku ofesi ya nthambi pasanafike pa 6 mwezi wotsatira. Ndiponso chonde onetsetsani kuti mwatenga malipoti onse a anthu amene akhala akulowa mu utumiki kuti tikhale ndi chiwerengero cholondola cha malipoti a utumiki wa kumunda. Zikuoneka kuti mipingo ina ikumatumiza malipoti otsika ku ofesi ya nthambi. Tikupereka malingaliro akuti alembi a mipingo aziwerenga mobwerezabwereza kalata ya pa February 13, 2004, yopita kwa alembi onse a mipingo asanalembe lipoti la mwezi. Kuti mutsimikizire kuti zonse zili bwino, ndi bwino kuti woyang’anira wotsogolera kapena ngati iye palibe, mkulu wina azionanso lipotilo lisanatumizidwe ku ofesi ya nthambi. Ndiponso muzigwiritsa ntchito envulopu yolembedwa kuti REPORT DESK kutumizira malipoti (S-1) basi.

◼ Mafomu Atsopano Omwe Alipo:

Kaonaneni ndi Wachidwi Uyu (S-43)—Chichewa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena