Konzani Zothandiza Okalamba
Mpingo wakale wachikristu unali ndi mayina a akazi amasiye amene anayenerera kuti athandizidwe. (1 Tim. 5:9, 10) Mofananamo lerolino, nthawi zina akulu angakhale ndi mayina a anthu odwala ndi okalamba amene akufunikira chisamaliro chapadera. M’mipingo ina, mkulu mmodzi amapatsidwa udindo wapadera woyang’anira ntchito imeneyi. Popeza kuti okalamba ambiri, ngati Naomi, sakhala omasuka kupempha thandizo, mkulu ameneyu afunikira luso kuti afufuze za zosowa zawo—mochenjera komanso mwaulemu—n’kutsimikizira kuti zonse zofunikira zachitika. Mwachitsanzo, angafunike kuona ngati pa Nyumba ya Ufumu pali zinthu zokwanira zimene odwala ndiponso okalamba angazifune. Mbale ameneyo angafunikirenso kuonetsetsa kuti onse amene sangathe kufika ku Nyumba ya Ufumu ayenderedwe ndi kulimbikitsidwa powafotokozera nkhani zomwe zakambidwa kumisonkhano.
Pangafunikirenso kukonza dongosolo labwino la momwe angamayendere popita ku misonkhano ya mpingo ndiponso ya chigawo. Mlongo wina wokalamba anali pavuto lakuti munthu amene ankamutenga popita kumisonkhano nthawi zonse anachokapo. Anaimba telefoni kwa anthu ambirimbiri asanapezeke wodzamutenga. Zimenezi zinachititsa mlongoyo kuganiza kuti anali mtolo kwa ena. Kukanakhala kuti zimenezi anakonza ndi mkulu, mlongoyo sakanavutika choncho. Mkuluyo angathenso kupempha mabanja osiyanasiyana kuti azilandirana poyendera okalamba. Potero ana nawonso angaphunzire kuti kusamalira okalamba ndi khalidwe labwino lachikristu. Ndi bwino kuti ana aphunzire kusenza udindo umenewu. (1 Tim. 5:4) Woyang’anira dera wina ananena kuti: “Ndaona kuti ndi ana kapena achinyamata ochepa kwambiri amene amakaona odwala kapena okalamba modzifunira.” Mwinamwake iwo saganizirako n’komwe, kapena sadziwa zoti anganene kapena kuchita. Makolo angawaphunzitse ana awo zinthu zimenezi.
Komano, kumbukirani kuti achikulire ambiri angayamikire ngati atadziwa mwamsanga kuti bwenzi lawo likubwera. Izi zimawapatsa chimwemwe chowonjezereka panthawi imene akuyembekeza mlendo. Ngati alendo abweretsa mphatso, monga sopo kapena chakudya, ndiyeno n’kuyeretsa malowo mwamsanga atamaliza, zimam’chepetsera ntchito wachikulireyo. Pofuna kuthandiza okalamba, mipingo yambiri imachita Phunziro la Buku la Mpingo masana. M’dera lina mabanja ena komanso ofalitsa osakwatira anapemphedwa kuti azipita ku phunziro longa limeneli, ndipo gulu la phunziro la bukulo linakhala ndi okalamba komanso achinyamata, onse otha kuthandizana. Musasiyire akulu okha mumpingo kuti ndiwo azichita zimenezi. Tonsefe tiyenera kukhala maso kuti tiziona zosowa za odwala ndiponso okalamba. Tingawapatse moni ku Nyumba ya Ufumu n’kucheza nawo. Iwo angakonde mutawaitana kunyumba kwanu kuti mucheze nawo. Anthu achikulire amafunika kuwathandiza kuti aone kuti sitikuwanyalanyaza. Musawalole kudzipatula kukhala paokha, monga momwe anafuna kuchitira Naomi, chifukwa kutero kungafulumizitse ukalamba wawo.
Ana olumala kapena odwala amafunikiranso kuwasamalira. Wa Mboni wina amene anali ndi ana atatu odwala matenda osachiritsika, amene awiri a iwo anamwalira, ananena kuti: “Zimakhala zovuta kuti mpingo upitirizebe kusamalira odwala amene angakhale akudwala kwa nthawi yaitali. Bwanji osasankha ofalitsa achinyamata odalirika amene angamakambirane lemba la tsiku ndiponso kumawerenga chaputala chimodzi m’Baibulo tsiku lililonse ndi mnzawo wodwalayo? Achinyamata, komanso apainiya, angamasinthane ndi anzawo pochita zimenezi.”
Udindo wa Tonse: Kusamalira odwala komanso okalamba ndi udindo waukulu zedi. Achibale a wodwala amalemedwa ndipo amapsinjika maganizo. Choncho m’poyenerera kuti mpingo wonse uziwamvetsetsa ndiponso kuwathandiza. Amene akusamalira odwala, kaya akhale achibale kapena okhulupirira anzawo, adziwe kuti akuchita bwino, ngakhale ngati akuphonya misonkhano ina kapena ngakhale maola a mu utumiki wa kumunda atachepa kwakanthawi. (Yerekezani ndi 1 Timoteo 5:8.) Angalimbikitsidwe ngati atadziwa kuti mpingo ukumvetsetsa zimene akukumana nazo. Nthawi zina mbale kapena mlongo angamulandireko amene akuyang’anira wodwalayo kotero kuti angathe kukapezeka kumsonkhano kapena kupita mu ulaliki kwa maola ochepa kuti alimbikitsidwe.
Tonsefe tiyenera kupitirizabe kulimbitsa chiyembekezo chathu chimene chingateteze maganizo athu monga chisoti, makamaka m’nthawi ya chiyeso. (1 Ates. 5:8) Tikuyang’ana kutsogolo ndi chidaliro komanso chiyembekezo champhamvu pamene sikudzakhalanso matenda kapena kufooka ndi ukalamba. Panthawiyo, aliyense adzakhala bwinobwino. Ngakhale akufa adzauka. (Yoh. 5:28, 29) Zinthu zosaoneka zimenezi tikuziona ndi maso achikhulupiriro. Musalole zimenezi kuchoka m’maganizo mwanu.—Yes. 25:8; 33:24; Chiv. 21:3, 4.