Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/05 tsamba 7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
km 9/05 tsamba 7

Zilengezo

◼ Mabuku ogawira mu September: Gawirani buku la Lambirani Mulungu Woona Yekha. Mipingo imene ili ndi mabuku kapena mabulosha ambiri akale ingathe kugawira amenewo. Tikukumbutsanso mipingo kumaitanitsiratu mabuku okwanira ogwiritsa ntchito mu utumiki monga mmene amasonyezera mu Utumiki Wathu wa Ufumu uliwonse. October: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Kwa amene aonetsa chidwi, agawireni bulosha la Mulungu Amafunanji. November: Gawirani buku la Phunzirani kwa Mphunzitsa Waluso. Ngati eni nyumba anena kuti alibe ana, gawirani buku la Chidziŵitso kapena thirakiti lakuti Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo? December: Gawirani buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako.

◼ Ofesi ya nthambi siisamalira oda ya mabuku ya wofalitsa aliyense payekha. Woyang’anira wotsogolera azikonza chilengezo mwezi uliwonse choti chiziperekedwa asanatumize ku nthambi oda ya mwezi ndi mwezi ya mpingo kuti onse amene akufuna mabuku auze mbale woyang’anira za mabuku. Chonde kumbukirani mabuku amene ali m’gulu la zofunsira mwapadera.

◼ Tikukumbutsa akulu kutsatira malangizo a mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 1991, masamba 21 mpaka 23 onena za ochotsedwa kapena odzilekanitsa amene angakhale ndi chidwi chofuna kubwezeretsedwa.

◼ Nkhani ya onse yapadera ya panyengo ya Chikumbutso cha 2006 idzakambidwa Lamlungu, pa April 30. Tidzalengeza mutu wa nkhaniyi m’tsogolo muno. Mipingo imene idzakhale ndi woyang’anira dera, msonkhano wadera, kapena tsiku la msonkhano wapadera mlungu umenewu, idzakhale ndi nkhani yapaderayi mlungu wotsatira. Mpingo wina uliwonse usadzakhale ndi nkhani yapaderayi lisanafike Lamlungu, pa April 30, 2006.

◼ Mwezi wa October udzakhala mwezi wabwino kwambiri kuchita upainiya wothandiza, chifukwa uli ndi mapeto a mlungu asanu athunthu.

◼ Mipingo iyambe kuitanitsa Lemba la Chaka cha 2006. Lemba la chaka lidzakalako m’Chichewa, Chingelezi ndi Chitumbuka. Mipingo iyenera kuitanitsa pepala limodzi la lemba la chaka basi pa chinenero chimodzi ndipo iyenera kuika lemba la chakalo m’Nyumba ya Ufumu podzafika pa January 1, 2006.

◼ Utumiki Wathu wa Ufumu wa August 2005 unasonyeza zofalitsa za m’Chiyao zimene zilipo. Mipingo imene ili ndi anthu m’gawo lawo amene angapindule ndi zofalitsa zimenezi iyenera kuitanitsa zinthuzi pa Fomu Yofunsira Mabuku (S-14).

◼ Vidiyokaseti Yatsopano Yomwe Ilipo:

Worship the Only True God—On Videocassette (Gawo 1-8) —Chinenero cha Manja cha ku America

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena