Zilengezo
◼ Magazini ogawira mwezi wa January: Gawirani kabuku kakuti Dikirani! February: Tidzagawira buku la Yandikirani kwa Yehova. March: Gawirani buku latsopano lija la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? April: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mukabwerera kwa anthu amene anachita chidwi, kuphatikizapo amene amapezeka pa chikumbutso kapena misonkhano ina koma sabwera kumisonkhano mokhazikika, muzikagawira makamaka buku latsopano la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Cholinga chanu chizikhala choyambitsa phunziro la Baibulo m’bukulo.
◼ Mwezi wa April ndi mwezi wabwino kwambiri kuchita upainiya wothandiza chifukwa choti uli ndi masiku asanu a Loweruka ndi Lamlungu.
◼ Kuyambira mu February mpaka kufika pa March 5, mutu wa nkhani ya onse ya oyang’anira madera udzakhala wakuti “Mungakhale Moyo Wamtendere Panopo Ndiponso Kwamuyaya.”
◼ Mipingo iyenera kukonzekera bwinobwino kudzachita Chikumbutso chaka chino Lachitatu, pa April 12, dzuwa litalowa. Nkhani ya Chikumbutso ingathe kuyamba msangako koma musayambe kuyendetsa zizindikiro mpaka dzuwa litalowa. Mverani zimene odziwa zanyengo anene zokhudza nthawi imene dzuwa lidzalowere kwanuko. Mpingo uliwonse uyenera kuyesetsa kuti ukhale ndi mwambo wake wa Chikumbutso. Komabe, nthawi zina zimenezi sizitheka. Ngati m’Nyumba ya Ufumu imodzi mumasonkhana mipingo ingapo, mpingo umodzi kapena mipingo inayo idzapeze malo ena ochitirako Chikumbutso. Ngati n’kotheka, pofuna kuti mipingo yonse ipindule bwinobwino ndi mwambowu, pazitha mphindi zosachepera 40 mpingo wotsatira usanayambe mwambo wawo wa chikumbutso.