Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/06 tsamba 7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
km 2/06 tsamba 7

Zilengezo

◼ Magazini ogawira mwezi wa February: Tidzagawira buku la Yandikirani kwa Yehova. March: Gawirani buku latsopano lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? April ndi May: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mukabwerera kwa anthu amene anachita chidwi, kuphatikizapo amene amapezeka pa chikumbutso kapena misonkhano ina koma sabwera kumisonkhano mokhazikika, muzikagawira makamaka buku latsopano lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Cholinga chanu chizikhala choyambitsa phunziro la Baibulo m’bukulo.

◼ Popeza kuti mwezi wa April uli ndi milungu isanu yathunthu, udzakhala mwezi wabwino kwambiri kuchita upainiya wothandiza.

◼ Nkhani ya onse yapadera ya nyengo ya Chikumbutso cha 2006 idzakhala ndi mutu wakuti “Kodi Mulungu Ndiye Akulamulirabe?” Onani zilengezo zofanana ndi zimenezi mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa September 2005.

◼ Pa Msonkhano wa Utumiki woyambira April 3, tidzakambirana nkhani ya pa tsamba 6 ya mutu wakuti “Sangalalani Pophunzira Buku Lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?” Chonde, sungani nkhani imeneyo ndi ndandanda yake yophunzirira.

◼ Woyang’anira wotsogolera kapena mbale wina wosankhidwa ndi iye ayenera kupanga oditi akaunti ya mpingo pa March 1 kapena mwamsanga pambuyo pake. Mukatsiriza kuchita oditi, muyenera kulengeza ku mpingo pamodzi ndi lipoti la maakaunti lotsatira.

◼ Mipingo ikukumbutsidwa kuona ngati ili ndi autilaini ya nkhani ya Chikumbutso, chimene chidzachitike Lachitatu, April 12. Autilaini yatsopano kwambiri ili ndi deti la 12/01. Ngati mipingo ikufuna autilaini yatsopano, iodetse mwa kugwiritsira ntchito Fomu Yofunsira Mabuku (S-14). Dziwani kuti ofesi yanthambi imasunga maautilaini a nkhani za ukwati ndi maliro. Mungaitanitsenso zimenezi pa Fomu Yofunsira Mabuku (S-14), ngati mungazifune.

◼ Mlembi ndi woyang’anira utumiki ayenera kuona ntchito ya apainiya okhazikika. Ngati ena zikuwavuta kukwanitsa maola awo, akulu ayenera kukonza zokumana nawo kuti awathandize. Kuti mupeze mfundo zina, werenganinso kalata ya pachaka ya S-201.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena