Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/06 tsamba 3
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
km 3/06 tsamba 3

Zilengezo

◼ Mabuku ogawira mwezi wa March: Gawirani buku latsopano lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? April ndi May: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mukabwerera kwa anthu amene anachita chidwi, kuphatikizapo amene amapezeka pa chikumbutso kapena misonkhano ina koma sabwera kumisonkhano mokhazikika, muzikagawira makamaka buku latsopano lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Cholinga chanu chizikhala choyambitsa phunziro la Baibulo m’bukulo. June: Gawirani buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Ngati anthu ena anena kuti alibe ana, gawirani buku la Chimwemwe cha Banja.

◼ Popeza mwezi wa April uli ndi masiku a Loweruka asanu ndi masiku a Lamlungu asanunso, udzakhala mwezi wabwino kwambiri kuchita upainiya.

◼ Chikumbutso chidzachitika Lachitatu pa April 12, 2006. Ngati mpingo wanu umakhala ndi misonkhano Lachitatu, muyenera kusintha n’kudzachita tsiku lina mlungu womwewu ngati Nyumba ya Ufumu sidzakhala ikugwiritsidwa ntchito. Ngati zimenezi n’zosatheka ndipo zakhudza Msonkhano wa Utumiki, mungathe kusankha nkhani zokhazo zimene zili zofunika kwambiri mu mpingo wanu n’kudzaziphatikiza ku Msonkhano wina wa Utumiki.

◼ Mipingo ifunika kuti izipereka kwa ofalitsa magazini atsopano a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! akangofika. Zimenezi zidzathandiza kuti ofalitsa athe kudziwiratu bwino nkhani zimene zili m’magaziniwo asanakawagawire mu utumiki wa kumunda. Mungathenso kupereka Utumiki Wathu wa Ufumu kwa ofalitsa ukangofika kudzera m’Maphunziro a Buku a Mpingo.

◼ Ofesi ya nthambi silembera wofalitsa oda ya mabuku amene akuwafuna. Woyang’anira wotsogolera azilengeza mwezi uliwonse asanatumize ku nthambi oda ya mwezi ndi mwezi ya mpingo kuti onse amene akufuna mabuku auze mbale woyang’anira za mabuku. Chonde, kumbukirani zofalitsa zimene zili za oda yapadera, kutanthauza kuti, mpingo uyenera kuitanitsa zimenezo kokha ngati pali anthu amene akuzifuna. Muzitumiza Fomu Yofunsira Mabuku (S-14) mwachangu mwezi uliwonse.

◼ Mawu kwa Alembi a Mpingo: Mukamadziwitsa ofesi ya nthambi za mabuku amene takutumizirani molakwitsa, muzikhala ndi ndandanda yolongedzera mabuku m’katoni pafupi ngati zingatheke. Ngati mukulemba kalata ku ofesi ya nthambi, muzitumizanso kope ya ndandanda yolongedzera mabuku.

◼ Zofalitsa Zatsopano Zomwe Zilipo:

Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?—Chichewa; Chifalansa; Chingelezi; Chiswahili; Chitumbuka.

Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?—Zilembo Zazikulu—Chichewa

Mavuto Onse a Anthu Adzatha Posachedwapa (Thirakiti Na. 27) —Chichewa; Chifalansa; Chingelezi; Chiswahili; Chitumbuka.

◼ Ma CD Atsopano Omwe Alipo:

Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?—Chifalansa; Chingelezi

◼ Makaseti Atsopano Omwe Alipo:

Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?—Chingelezi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena