Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/06 tsamba 3
  • Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
km 4/06 tsamba 3

Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

“CHISOMO kwa inu, ndi mtendere wochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Kristu.” Amenewa ndi mawu amene Paulo ankakonda kulemba m’makalata ake ochuluka opita ku mipingo. Mawuwa akufotokoza bwino kwambiri zimene zili kumtima kwathu pokufunirani mafuno abwino.—Aef. 1:2.

Timayamikiradi kwambiri chisomo chimene Yehova anasonyeza kupyolera mu nsembe ya dipo ya Kristu Yesu. Chifukwa cha dipo limeneli, tili ovomerezeka pamaso pa Mulungu. Zimenezi sizikanatheka ndi khama lathu kaya titaphunzira Baibulo mwa khama bwanji, kaya titalalikira uthenga wabwino kwambiri bwanji, kayanso titachita ntchito zabwino zotani. Kukhululukidwa machimo ndiponso moyo wosatha zapatsidwa kwa ife, osati ngati malipiro chifukwa cha khama lathu ayi, koma monga mphatso zosonyeza chisomo cha Yehova kudzera mwa Yesu Kristu.—Aroma 11:6.

Paulo analembera okhulupirira anzake kalatayi kuti: Tikudandaulirani “kuti musalandire chisomo cha Mulungu kwachabe inu, (pakuti anena, m’nyengo yolandiridwa ndinamva iwe, ndipo m’tsiku la chipulumutso ndinakuthandiza; taonani, tsopano ndiyo nyengo yabwino yolandiridwa, taonani, tsopano ndilo tsiku la chipulumutso).” Kalelo Yerusalemu asanawonongedwe, ‘nyengo yolandiridwa’ imeneyi inalipodi. Anthu oona mtima amene ankakondadi Yehova anapulumutsidwa mwauzimu. Zimenezi zinachititsa kuti potsirizira pake anthu okhulupirika amenewo apulumuke atathawa mu Yerusalemu, mzindawo utatsala pang’ono kuwonongedwa m’chaka cha 70 C.E.—2 Akor. 6:1, 2.

Masiku anonso, tikukhala “m’nyengo yolandiridwa” komanso “m’tsiku la chipulumutso.” Onse amene Yehova akuwavomereza kukhala atumiki ake, amenenso akuwapulumutsa mwauzimu, akuyembekezera kudzapulumuka “tsiku lalikulu la Yehova” limene tsopano layandikira kwambiri.—Zef. 1:14.

Kuyandikira kwa tsiku la Yehova kwatipatsa ntchito yaikulu kwambiri. Tiyenera kuchenjeza anthu za kuyandikira kwa tsiku limeneli ndiponso kuthandiza anthu oona mtima kuti apindule ndi chisomo cha Yehova kuti nawonso adzapulumuke. Paulo ankaona kuti ntchito imeneyi ndi yofunika kwambiri. N’chifukwa chake analemba kuti: “Tsoka ine ngati sindilalikira Uthenga Wabwino.” Anafotokozanso mmene ankamvera mu mtima ndi mawu awa: “Ine ndili wamangawa . . . wa anzeru ndi wa opusa. Chotero, momwe ndingakhoze ine, ndilikufuna kulalikira uthenga wabwino.”—1 Akor. 9:16; Aroma 1:14, 15.

Yehova adzatiimba mlandu ngati tinyalanyaza ntchito yofunika kwambiri yochenjeza anthu imeneyi. Tikudziwa zimene Yehova anauza mneneri Ezekieli: “Wobadwa ndi munthu iwe, ndakuika ukhale mlonda wa nyumba ya Israyeli, m’mwemo mvera mawu otuluka m’kamwa mwanga, nundichenjezere iwo. Ndikanena kwa woipa, Udzafa ndithu, koma iwe osam’chenjeza, wosanena kum’chenjeza woipayo aleke njira yake yoipa, kum’sunga ndi moyo, woipa yemweyo adzafa mu mphulupulu yake; koma mwazi wake ndidzaufuna pa dzanja lako.”—Ezek. 3:17, 18.

Masiku otsiriza ano ndi ovuta kwambiri. Sizophweka kusamalira bwinobwino banja, ntchito, zochita za kumpingo, ndiponso kulalikira. Mwinanso ambirinu ndinu opsinjika maganizo chifukwa cha matenda, nkhawa, ukalamba, kapenanso chitsutso. Ambirinu mwalema. Tikufuna kukuuzani kuti timakumverani chifundo, mogwirizana ndi mawu a Yesu akuti: “Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu.” (Mat. 11:28) Tikufunanso kukuyamikirani nonse amene mukuyesetsa kupitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika ngakhale kuti mwakumana ndi mavuto aakulu ndi aang’ono omwe.

Chifukwa cha changu chanu pa ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa ndiponso chifukwa cha madalitso a Yehova, anthu okwanira pafupifupi 4,762 amabatizidwa mlungu uliwonse padziko lonse lapansi. Chaka cha utumiki chathachi, kunapangidwa mipingo yatsopano yokwana 1,375. Tikuyembekezera ndiponso tikupemphera kuti buku latsopano lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? limene lili kale mu zinenero zoposa 120, lidzathandiza anthu mamiliyoni ambiri kupindula ndi chisomo ndiponso mtendere wochokera kwa Yehova “m’tsiku la chipulumutso” lino.

Dziwani kuti Bungwe Lolamulira limakukondani kwambiri ndipo timakupemphererani. Tikukuyamikaninso chifukwa chakuti mumatipempherera.

Ndife abale anu,

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena