Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira April 24, 2006. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya March 6 mpaka April 24, 2006. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 30. [Dziwani izi: Pa funso lomwe kumapeto kwake silikusonyeza buku lililonse lomwe mwatengedwa nkhaniyo, ndiye kuti muyenera mufufuze nokha kuti mupeze mayankho ake.—Onani buku la Sukulu ya Utumiki, mas. 36-7.]
LUSO LA KULANKHULA
1. Tikamaphunzitsa, n’chifukwa chiyani tiyenera kupuma nthawi iliyonse yomwe tikusintha ganizo, koma n’chiyani chimene chingatilepheretse kuchita zimenezi? [be-CN tsa. 98 ndime 2 ndi 3]
2. N’chifukwa chiyani tifunika kupuma tikamalalikira ena? [be-CN tsa. 99 ndime 5 mpaka tsa. 100 ndime 3]
3. N’chifukwa chiyani kutsindika ganizo n’kofunika pokamba nkhani, ndipo tingathe bwanji kutsindika ganizo moyenerera? [be-CN tsa. 101 ndime 1 mpaka 5, bokosi]
4. Tikamawerenga pamaso pa anthu, kodi tingatsimikize bwanji kuti malingaliro ofunika kwambiri a nkhani yathu agogomezeredwa? [be-CN tsa. 105 ndime 1 mpaka 6]
5. N’chifukwa chiyani mphamvu ya mawu yoyenerera ili yofunika pophunzitsa, ndipo tingadziwe bwanji kukula kwa mphamvu ya mawu yoti tigwiritse ntchito? [be-CN mas. 107 mpaka 108]
NKHANI NA. 1
6. Kodi ndani amene ali “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wotchulidwa pa Mateyu 24:43-47? [od-CN tsa. 16]
7. Pamene Solomo ananena kuti “zonse zinali zachabechabe ndi kungosautsa mtima,” kodi anali kufotokoza chiyani? (Mlal. 2:11) [w04-CN 10/15 tsa. 4 ndime 3 mpaka 4]
8. Kodi tingakulitse bwanji kukonda Mulungu? (Marko 12:30) [w04-CN 3/1 mas. 19 mpaka 21]
9. Kodi zinthu zauzimu zimasiyana bwanji ndi kukonda chuma? [w04-CN 10/15 mas. 5 mpaka 7]
10. Kodi n’chiyani chimene chingatithandize kumvetsera pamisonkhano ikuluikulu popanda kudodometsedwa? [be-CN mas. 15 mpaka 16]
KUWERENGA BAIBULO KWA MLUNGU NDI MLUNGU
11. N’chifukwa chiyani nkhope ya Hamani inaphimbidwa? (Estere 7:8)
12. Kodi ndi mzimu wotani umene unasokoneza maganizo a Elifazi? (Yobu 4:15, 16) [w05-CN 9/15 tsa. 26 ndime 2]
13. Kodi mawu a Yobu olembedwa pa Yobu 7:9, 10 ndi Yobu 10:21 amasonyeza kuti sanakhulupirire za kuuka kwa akufa?
14. Kodi Yobu anatanthauzanji ndi mawu akuti “ndapulumuka ndili nazo nkhama za mano anga [“khungu la mano anga,” NW]”? (Yobu 19:20)