Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu March: Gawirani buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani ndipo yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo. April ndi May: Tidzagawira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mukamachita maulendo obwereza kwa anthu achidwi, ngakhalenso amene anafika pa Chikumbutso kapenanso pa misonkhano ina koma safika pa misonkhano ya mpingo nthawi zonse, yesetsani kuwagawira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani, ndi cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo. June: Mungathe kugawira buku la Creator kapena la Chimwemwe cha Banja.
◼ Mipingo ifunika kuti izipereka kwa ofalitsa magazini atsopano a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! akangofika. Zimenezi zidzathandiza kuti ofalitsa athe kudziwiratu bwino nkhani zimene zili m’magaziniwo asanagawire mu utumiki wa kumunda.
◼ Woyang’anira wotsogolera kapena wina amene iye wam’sankha awerengere maakaunti a mpingo a miyezi ya December, January, ndi February. Mukatha kuwerengerako, lengezani kumpingo pamodzi ndi lipoti lotsatira la maakaunti.—Onani Malangizo Oyendetsera Maakaunti a Mpingo (S-27).
◼ Ofesi ya nthambi silembera wofalitsa oda ya mabuku amene akuwafuna. Ofalitsa ayenera kuitanitsa mabuku omwe akuwafuna kudzera kumpingo. Woyang’anira wotsogolera azikonza zoti mwezi uliwonse asanatumize ku nthambi oda ya mwezi ndi mwezi ya mpingo pakhale chilengezo kuti onse amene akufuna mabuku auze mbale woyang’anira za mabuku. Chonde, kumbukirani zofalitsa zimene zili za oda yapadera, kutanthauza kuti, mpingo uyenera kuitanitsa zimenezo pokhapokha ngati pali anthu amene akuzifuna. Muzitumiza Fomu Yofunsira Mabuku (S-14) mwachangu mwezi uliwonse.
◼ Mipingo iyambe kuitanitsa mabaundi voliyumu a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! a 2006. Mabaundi voliyumuwa adzakhalapo m’Chingelezi ndi Chifalansa. Mabaundi voliyumuwa azidzaonekera monga zoyembekezeredwa pa mipambo yolongedzera katundu wa mipingo kufikira pamene adzayambe kupezeka ndi kutumizidwa. Mabaundi voliyumu ndi zinthu za oda yapadera.
◼ Atumiki a Mabuku adziwe kuti seti ya maabamu asanu ya Sing Praises on Cassette (csLsb-E) yogwiritsa ntchito pamisonkhano ya mpingo siizipezekanso moti mpingo n’kuitanitsa. M’malo mwake aziitanitsa seti ya ma CD 8 ya Sing Praises on CD (cdsb-E). Komabe, padakali makaseti ochepa (a nyimbo Nambala 1 mpaka 225) omwe angaitanitse kuti alowe m’malo mwa ena. Makasetiwa akadzatha, sizidzathekanso kuitanitsa makaseti amenewa.
◼ Mabuku atsopano amene alipo:
Live With Jehovah’s Day in Mind (jd)—Chingelezi, Chifalansa ndi Chiswahili
Dikirani! (kp)—Chilomwe
Kodi Mulungu Amatisamaliradi? (dg)—Chitumbuka