Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu May: Tidzagawira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mukamachita maulendo obwereza kwa anthu achidwi, ngakhalenso amene anafika pa Chikumbutso kapenanso pamisonkhano ina koma safika pa misonkhano ya mpingo nthawi zonse, yesetsani kuwagawira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani, ndi cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo. June: Gawirani buku la Chimwemwe cha Banja. July ndi August: Gwiritsani ntchito kalikonse ka timabuku tamasamba 32 totsatirati: Dikirani!, Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi?, Njira ya ku Moyo Wosatha—Kodi Mwaipeza?, ndi Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira.
◼ Macheke a zopereka za ntchito ya padziko lonse operekedwa pa msonkhano wachigawo ndiponso otumizidwa ku ofesi ya nthambi, azilembedwa kuti ndalamazo apatse “Watch Tower.” Adiresi ya ofesi yoona za ndalama ya ku nthambi ndi iyi: Watch Tower Bible and Tract Society, P. O. Box 30749, Lilongwe 3.
◼ M’mbuyo monsemu, mipingo yakhala ikuitanitsa Mabaibulo a The Emphatic Diaglott (di-E) ndi The Kingdom Interlinear Translation of the Greek Scriptures (int-E). Koma tsopano, dziwani kuti Maibulo a The Emphatic Diaglott (di-E) sazipezekanso. Motero kuyamba panopa muzingoitanitsa Baibulo la The Kingdom Interlinear Translation of the Greek Scriptures (int-E) lokha basi.
◼ Mlungu woyambira September 24 tidzayamba kuwerenga buku la m’Baibulo la Danieli, pa kuwerenga Baibulo kwa mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Ndibwino kugwiritsa ntchito buku la Ulosi wa Danieli ndi mabuku ena pofufuza mfundo zina ndi zina. Ngati ena akufuna mabukuwa aodetse kudzera ku mpingo pogwiritsira ntchito Fomu Yofunsira Mabuku (S-14).
◼ Ma CD atsopano amene alipo ndi awa:
Sing Praises to Jehovah—MP3 (mpsb-E)—Chingelezi
◼ Mabuku amene adakalipobe:
2004 Yearbook of Jehovah’s Witnesses—Chingelezi
2005 Yearbook of Jehovah’s Witnesses—Chingelezi, Chifalansa ndi Chiswahili
2006 Yearbook of Jehovah’s Witnesses—Chiswahili