Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 8/07 tsamba 7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
km 8/07 tsamba 7

Zilengezo

◼ Mabuku ogawira mu August: Mungagwiritse ntchito kalikonse ka timabuku tamasamba 32 iti: Dikirani!, Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi?, Njira ya ku Moyo Wosatha—Kodi Mwaipeza?, ndi Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. September: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Yesetsani kwambiri kuyambitsa phunziro la Baibulo paulendo wanu woyamba. Ngati mwininyumba ali nalo kale bukuli, mum’sonyeze mmene angapindulire nalo mwa kupanga naye mwachidule phunziro la Baibulo. October: Magazini ya Nsanja ya Olonda ndi ya Galamukani! Mukabwerera kwa anthu amene anachita chidwi, agawireni ndi kukambirana nawo za m’kapepala ka Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo? Chitani zimenezi ndi cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo. November: Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Ngati anthu anena kuti alibe ana, gawirani kabuku kakuti Dikirani!

◼ Mwezi wa September ndi mwezi wabwino kwambiri kuchita upainiya wothandiza chifukwa choti uli ndi masiku asanu a Loweruka ndi Lamlungu.

◼ Mipingo iyambe kuitanitsa Kalendala ya 2008 ya Mboni za Yehova ndi Yearbook of Jehovah’s Witnesses ya 2008 potumiza oda yawo yotsatira ya mabuku. Makalendala adzakhalapo m’Chichewa, Chingelezi, Chifalansa ndi Chiswahili, ndipo Yearbook idzakhalapo m’Chingelezi, Chifalansa ndi Chiswahili. Zinthu zimenezi ndi zinthu za oda yapadera, motero muyenera kuziitanitsa ngati pali anthu amene akuzifuna. Zinthuzi zizidzalembedwa kuti “Zoyembekezeredwa” pa mipambo yolongedzera mpaka pamene zidzayambe kupezeka. Muyenera kulengeza kumpingo kuti mukuoda zinthu zimenezi musanatumize oda. Ofalitsa asachedwe kuodetsa zinthuzi pamalo olembetsera mabuku ndipo mlembi asachedwe kutumiza odayo ku ofesi ya nthambi. Woyang’anira wotsogolera aonetsetse kuti maoda asatumizidwe mochedwa. Ndipo kukonzekera pasadakhale n’kofunika. Palibe dongosolo lapadera loti zinthuzo zingafike mofulumira mukaitanitsa mochedwa. Woyang’anira utumiki ayenera kuonetsetsa kuti mpingo ukuitanitsa kokha mabuku omwe udzagwiritsire ntchito, ndipo akachita zimenezi adzapewa kuitanitsa mabuku ochuluka.

◼ Mipingo sifunikira kuitanitsa kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku ka 2008 chifukwa timabukuti tidzatumizidwa mogwirizana ndi chiwerengero ndiponso chinenero cha Utumiki Wathu wa Ufumu umene mumalandira. Koma mipingo ikafuna timabuku tina towonjezera, iyenera kutumiza oda. Ndipo muyenera kulemba pa Fomu Yofunsira Mabuku (S-14) kuti, “Timabuku timene taitanitsa ndi towonjezera pa chiwerengero chimene tili nacho kale.” Mukalephera kuchita zimenezi simungalandire oda yanu. Timabuku ta Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku tidzakhalapo m’Chichewa, Chingelezi, Chifalansa, Chiswahili ndi Chitumbuka.

◼ Akulu akukumbutsidwa kuti atsatire malangizo amene anaperekedwa mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 1991, masamba 21 mpaka 23, onena za anthu alionse ochotsedwa kapena odzilekanitsa amene angafune kubwezeretsedwa.

◼ Mabuku Atsopano Amene Alipo:

Watch Tower Publications Index 2006 (dx06)—Chingelezi

◼ Ma DVD Atsopano Omwe Alipo:

Album for The Watchtower Announcing Jehovah’s Kingdom (dvcw07)

—Chinenero cha Manja cha ku America

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena