Tiyeni Tipitirize Kukhala Achangu Muutumiki
1 Kuyambira mu 1992, Mboni za Yehova zakhala zikutha maola oposa 1 biliyoni chaka chilichonse pantchito ya padziko lonse yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira. Ndife osangalala kwambiri kuti tathandizira nawo kuti zimenezi zitheke.—Mat. 28:19, 20.
2 Koma ulemu wonse ndi chitamando zipite kwa Yehova, chifukwa ndiye watichirikiza kuchita utumiki umenewu ‘m’nthawi yovuta’ ino. (2 Tim. 3:1) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikhalebe achangu mu ntchito yofunika kwambiri imeneyi?
3 Kodi Chimatipatsa Changu Choterocho ndi Chiyani? Timakhala achangu mu utumiki wa Ufumu chifukwa chakuti timakonda kwambiri Mulungu ndi anthu anzathu, komanso chifukwa chakuti ndife ofunitsitsa kukhala ndi moyo wogwirizana ndi kudzipereka kwathu kwa Mulungu. (Mat. 22:37-39; 1 Yoh. 5:3) Chikondi n’chimene chimatilimbikitsa kudzimana zinthu zina kuti tichite zambiri mu ntchito yolalikira imeneyi.—Luka 9:23.
4 Tichite Khama Kuti Tikhalebe Achangu: Mdani wathu Mdyerekezi akuchita chilichonse chomwe angathe kuti afooketse changu chathu mu utumiki. Zina mwa zimene iye akugwiritsa ntchito kuti atilefule ndizo kusalabadira kwa anthu m’gawo lathu, zokopa za dzikoli, mavuto a moyo watsiku ndi tsiku, ndi nkhawa zobwera chifukwa cha kufooka kwa thupi lathu.
5 Choncho tiyenera kuchita khama kuti tipitirizebe kukhala achangu. M’pofunika kukulitsa ‘chikondi chimene tinali nacho poyamba.’ Kuti tichite zimenezi, tifunika kuwerenga ndi kusinkhasinkha Mawu a Mulungu, Baibulo, ndi kugwiritsa ntchito bwino zinthu zonse zauzimu zimene “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amatipatsa.—Chiv. 2:4; Mat. 24:45; Sal. 119:97.
6 Monga momwe ulosi wa m’Baibulo umasonyezera, tsiku la Yehova lodzawononga anthu oipa likubwera mofulumira. (2 Pet. 2:3; 3:10) Pokumbukira zimenezi, tiyeni tikhale achangu muutumiki, ndi kuchita zambiri mu ntchito ya padziko lonse yolengeza Ufumu ndi kupanga ophunzira yomwe ili m’kati panopa.