Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu January: Gawirani kabuku kakuti Dikirani! February: Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. March: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo. April: Tidzagawira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Tidzayesetse kuyendera anthu atsopano achidwi amene anafika pa Chikumbutso ndiponso pankhani ya onse yapadera koma safika pa misonkhano ya mpingo nthawi zonse. Cholinga cha maulendo amenewa ndi kuyambitsa maphunziro a Baibulo ndi anthu amene sanayambe kuphunzira.
◼ Mwezi wa March ndi mwezi wabwino kwambiri kuchita upainiya wothandiza chifukwa choti uli ndi masiku asanu a Loweruka ndi Lamlungu.
◼ Kuyambira mu February mpaka kufika pa March 2, oyang’anira dera adzayamba kukamba nkhani ya onse yatsopano yakuti “Kodi Tingapeze Kuti Chithandizo Panthawi ya Mavuto?”
◼ Mipingo iyenera kukonzekera bwinobwino kudzachita Chikumbutso chaka chino Loweruka, pa March 22, dzuwa litalowa. Nkhani ya Chikumbutso ingathe kuyamba dzuwa lisanalowe koma musayambe kuyendetsa zizindikiro dzuwa lisanalowe. Fufuzani kwa odziwa zanyengo nthawi imene dzuwa lidzalowere kwanuko. Mpingo uliwonse uyenera kuyesetsa kuti ukhale ndi mwambo wakewake wa Chikumbutso. Komabe, nthawi zina zimenezi sizingatheke. Ngati m’Nyumba ya Ufumu yanu mumasonkhana mipingo ingapo, mpingo kapena mipingo inayo ingathe kupeza malo ena ochitirako Chikumbutso. Ngati n’kotheka, pofuna kuti aliyense adzapindule ndi macheza pambuyo pa Chikumbutso, pazitha mphindi zosachepera 40 mpingo wotsatira usanayambe mwambo wawo wa Chikumbutso. Bungwe la akulu liyenera kuganizira za makonzedwe amene angakhale bwino kwawoko.
◼ Mlembi wa mpingo ayenera kuonetsetsa kuti ali ndi kalata yotsimikiza kuikidwa kwa mpainiya (S-202) ya mpainiya aliyense wokhazikika wa mu mpingo wawo. Ngati alibe, ayenera kudziwitsa ofesi ya nthambi polemba kalata.
◼ Kuyambira mlungu wa August 4, 2008 tidzayamba kuphunzira buku la Yandikirani kwa Yehova pa Phunziro la Buku la Mpingo.
◼ Madalaivala a galimoto zosiya mabuku auzidwa kuti asamatenge makalata a anthu kupititsa ku mpingo kapena malo ena osiyako mabuku. Tachita izi n’cholinga chakuti chakudya chauzimu chizifika ku mipingo panthawi yake ndiponso kuti makalata opita ku nthambi azifika panthawi yake. Komabe angathe kutenga makalata a anthu amene ali mu utumiki wapadera wa nthawi zonse.
◼ Woyang’anira wotsogolera ayenera kuonetsetsa kuti amalandira Utumiki Wathu wa Ufumu wokwanira ndi wina pang’ono wowonjezera. Ngati akulandira wambiri, mpingo uyenera kuchepetsa chiwerengerocho pogwiritsa ntchito Fomu ya Maoda a Magazini. (M-202) Ngati akulandira wochepa kwambiri, angathenso kuwonjezera chiwerengerocho. Wofalitsa aliyense azilandira Utumiki Wathu wa Ufumu. Anthu amene amafika nthawi zonse pa Msonkhano wa Utumiki ndiponso amene atsala pang’ono kuyamba kuchita nawo utumiki wakumunda ayeneranso kulandira. Onetsetsani kuti mwasunga umodzi woika pa laibulale ya pa Nyumba ya Ufumu. Anthu ochotsedwa sayenera kupatsidwa Utumiki Wathu wa Ufumu. (Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa February 1987.)
◼ Monga tinalengezera mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa December, vidiyo yatsopano yakuti Pursue Goals That Honor God-On DVD (dvpsg) tsopano yayamba kupezeka. Vidiyoyi yapangidwa kuchokera m’sewero la pamsonkhano wachigawo wa mu 2005 ndipo ikusonyeza mavuto amene achinyamata amakumana nawo pamene akuyesetsa kukwaniritsa cholinga chawo chotumikira Mulungu. M’seweroli Timoteyo akuthandiza m’bale wachinyamata kuti asasinthe cholinga chake mwa kum’fotokozera mavuto amene anakumana nawo pofuna kukwaniritsa cholinga chake chochita utumiki wa nthawi zonse. Komanso, achinyamata angaone kuti si iwo okha amene nthawi zina amavutika ndi zofuna za makolo kapena anzawo omwe si Mboni. Angathenso kuona cholinga cha Timoteyo yemwe ankalimbikitsidwa kwambiri ndi mtumwi Paulo. DVD imeneyi ingathandize achinyamata kukonda choonadi komanso kukhala ndi cholinga chochita utumiki wa nthawi zonse. Pakalipano vidiyoyi ili m’Chingelezi mokha, koma m’tsogolo muno idzatuluka pa DVD ya zinenero zingapo.