Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 10/08 tsamba 7
  • Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
km 10/08 tsamba 7

Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Mafunso otsatirawa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira October 27, 2008. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya September 1 mpaka October 27, 2008. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 30.

LUSO LA KULANKHULA

1. Kodi tingadziwe bwanji chifukwa chimene anthu amakhulupirira zimene amakhulupirirazo? [be-CN tsa. 259 ndime 1, 2]

2. Kodi tingathandize bwanji munthu kuchotsa maganizo a tsankho kapena udani mumtima mwake? [be-CN tsa. 260 ndime 2]

3. Kodi tingathandize bwanji ophunzira athu kufufuza mtima wawo kuti athe kupita patsogolo mwauzimu? [be-CN tsa. 261 ndime 2]

4. Kodi tiyenera kukumbukira chiyani pamene tikuyesetsa kuwafika pa mtima omvera athu? [be-CN tsa. 262 ndime 3]

5. Kodi n’chifukwa chiyani tifunika kusunga nthawi pamisonkhano ya mpingo? [be-CN tsa. 263 ndime 1, 3, bokosi]

NKHANI NA. 1

6. Kodi n’chifukwa chiyani atumiki odzipereka a Yehova afunika kukhala ndi zolinga zauzimu? [od-CN tsa. 117 ndime 1]

7. Kodi ndani amene ali ndi udindo wopereka ndalama zosamalira Nyumba ya Ufumu iliyonse, ndipo amatsatira njira iti ya m’Malemba pochita zimenezi? [od-CN tsa. 121 ndime 1]

8. Kodi ndi ‘kulinganiza’ kotani kumene kukuchitika masiku ano pankhani yomanga Nyumba za Ufumu ndi Nyumba za Misonkhano? [od-CN tsa. 124 ndime 1]

9. Kodi pamakhala dongosolo lotani ngati ndalama zoyendetsera misonkhano yadera ndi masiku a msonkhano wapadera zaperewera? [od-CN tsa. 130 ndime 2]

10. Kodi n’chifukwa chiyani ofalitsa amalimbikitsidwa kugawira Mabaibulo ndi mabuku ofotokoza za m’Baibulo mu utumiki wawo, ndipo kodi abale oyang’anira mabuku a mpingo ayenera kuuona bwanji udindo wawo? [od-CN tsa. 133 ndime 1, 2]

KUWERENGA BAIBULO KWA MLUNGU NDI MLUNGU

11. Kodi ‘kum’pereka munthu [woipa] kwa Satana kuti thupilo liwonongedwe, kotero kuti mzimuwo upulumutsidwe,’ kumatanthauza chiyani? (1 Akor. 5:5) [w08-CN 7/15 “Mawu a Yehova ndi Amoyo—Mfundo Zazikulu za M’makalata a ku Korinto”]

12. Kodi mwambo wokumbukira imfa ya Yesu uyenera kuchitika kangati ndiponso “mpaka” liti? (1 Akor. 11:26) [w08-CN 7/15 “Mawu a Yehova Ndi Amoyo—Mfundo Zazikulu za M’makalata a ku Korinto”]

13. Kodi lemba la 2 Akorinto 12:2-4, likunena za masomphenya otani, ndipo kodi ndani amene ayenera kuti anaona masomphenyawa? [w04-CN 10/15 tsa. 8 ndime 4; tsa. 10 ndime 9]

14. N’chifukwa chiyani Paulo anayerekezera Chilamulo cha Mose ndi “namkungwi wotitsogolera kwa Khristu”? (Agal. 3:24) [w08-CN 3/1 mas. 18-21]

15. Kodi Paulo anatanthauza chiyani pamene anapemphera kuti “mzimu wanu, moyo wanu, ndi thupi lanu abale, zisungidwe”? (1 Ates. 5:23) [w08-CN 9/15 “Mawu a Yehova ndi Amoyo—Mfundo Zazikulu za M’makalata Opita kwa Atesalonika ndi Timoteyo”]

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena