Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira October 27, 2008. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya September 1 mpaka October 27, 2008. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 30.
LUSO LA KULANKHULA
1. N’chifukwa chiyani tiyenera kulimbikitsa ena “mwachikondi”? (Filem. 9) [be-CN tsa. 266 ndime 1-3]
2. Kodi tingatani kuti tithandize ena kukhala olimba mtima? [be-CN tsa. 268 ndime 4–tsa. 269 ndime 2]
NKHANI NA. 1
3. Tingasonyeze bwanji kuti timafunitsitsa kutsatira miyezo ya Yehova ya makhalidwe oyera ndi olungama? [od-CN tsa. 136 ndime 2]
4. N’chifukwa chiyani anthu ambiri masiku ano sazindikira ndiponso satsatira mfundo yolemekeza mutu? [od-CN tsa. 159 ndime 3])
5. N’chifukwa chiyani tonsefe tiyenera kupempherera abale athu tsiku lililonse? [od-CN tsa. 167 ndime 2]
KUWERENGA BAIBULO KWA MLUNGU NDI MLUNGU
6. Pa Tito 2:3, n’chifukwa chiyani Paulo anasonyeza kuti pali mgwirizano pakati pa “amiseche” ndi “akapolo a vinyo wambiri”? [w94-CN 6/15 tsa. 20 ndime 12]
7. Kodi mawu akuti Satana “ali ndi njira yochititsa imfa” amasonyeza kuti angathe kupha munthu aliyense amene akufuna? (Aheb. 2:14) [w08-CN 10/15 Mawu a Yehova Ndi Amoyo—Mfundo Zazikulu za M’makalata Opita kwa Tito, Filemoni, ndi Aheberi]
8. Kodi ‘wochita naye chipangano waumunthu’ m’chipangano chatsopano ndani? (Aheb. 9:16) [w08-CN 10/15 Mawu a Yehova Ndi Amoyo—Mfundo Zazikulu za M’makalata Opita kwa Tito, Filemoni, ndi Aheberi]
9. Kodi kukhala amtendere kumatanthauza chiyani, ndipo tiyenera kudzifunsa mafunso ati pankhani imeneyi? (Yak. 3:17) [w08-CN 3/15 tsa. 25 ndime 18]
10. Kodi mawu akuti “Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu” amatanthauza chiyani? (1 Yoh. 3:20) [w05-CN 8/1 tsa. 30 ndime 19]