Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu February: Gawirani mabuku otsatirawa ngati muli nawo: Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. March: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo. April ndi May: Tidzagawira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mukamachita maulendo obwereza kwa anthu achidwi, ngakhalenso amene anafika pa Chikumbutso kapenanso pa misonkhano ina koma safika pa misonkhano ya mpingo nthawi zonse, yesetsani kuwagawira buku latsopano la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? ndi cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo.
◼ Nkhani ya onse yapadera ya nyengo ya Chikumbutso ya 2009 ili ndi mutu wakuti “Kodi Mulungu Amaona Kuti Pali Chipembedzo Chimodzi Chokha Choona?” Onani chilengezo chofanana ndi chimenechi mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa September 2008.