Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/09 tsamba 3
  • Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
km 4/09 tsamba 3

Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Mafunso otsatirawa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira April 27, 2009. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya March 2 mpaka April 27, 2009. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 20.

1. Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Yosefe anachita polimbana ndi chiyeso chimene ankakumana nacho tsiku ndi tsiku? (Gen. 39:9) [w04-CN 1/15 tsa. 29]

2. Kodi Baibulo limasonyeza chiyani pankhani ya zikondwerero za tsiku la kubadwa? (Gen. 40:20-22) [rs-CN tsa. 362 ndime 1–tsa. 363 ndime 1]

3. Kodi n’chifukwa chiyani Yosefe ndi chitsanzo chabwino kwambiri pankhani yokhululukira amene atilakwira? (Gen. 45:4, 5) [w99-CN 1/1 tsa. 31 ndime 2-3]

4. Kodi mawu a Yosefe akuti ‘Mudzakwere nawo mafupa anga kuchokera kuno,’ anali ndi phindu lotani? (Gen. 50:25) [w07-CN 6/1 tsa. 28 ndime 10]

5. Kodi n’chiyani chingatithandize kusadzikayikira tikapatsidwa ntchito yovuta? (Eks. 4:10, 13) [w04-CN 3/15 tsa. 25 ndime 4]

6. Kodi njira imene Yehova anachitira ndi Farao inali ndi zotsatira zotani, ndipo kodi zimenezi zimatikhudza bwanji? (Eks. 9:13-16) [w05-CN 5/15 tsa. 21 ndime 8]

7. Kodi lemba la Eksodo 14:30, 31 lidzakwaniritsidwa bwanji m’nthawi yathu? [w04-CN 3/15 tsa. 26 ndime 5]

8. Kodi lemba la Eksodo 16:1-3 limasonyeza kuti kung’ung’udza n’koopsa bwanji? [w93-CN 3/15 tsa. 21 ndime 1-3]

9. Malinga ndi mfundo za Pangano la Chilamulo zopezeka pa Eksodo 19:5, 6, kodi Aisiraeli anatchedwa ‘ufumu wa ansembe, ndi mtundu wopatulika’ chifukwa chiyani? [w95-CN 7/1 tsa. 16 ndime 8]

10. Kodi lamulo la nambala 10 lonena za kusirira limaposa bwanji malamulo a anthu? (Eks. 20:17) [w06-CN 6/15 tsa. 23-24 ndime 16]

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena