Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu June: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? July ndi August: Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? ndi Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. September: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Ngati n’kotheka ofalitsa aziyesetsa kuyambitsa maphunziro a Baibulo paulendo woyamba umene agawira bukulo.
◼ Baibulo la Revised Nyanja (Union) Version silipangidwa ndi gulu la Yehova ndipo amachita kugula. Popeza mtengo wa Baibulo limeneli ndi woposa K1,000.00, limatumizidwa kwa ofalitsa obatizidwa ndi osabatizidwa ndiponso ophunzira Baibulo opita patsogolo okha basi, amene alibe Baibulo komanso ngati aitanitsa mwapadera. Anthu oyenerera kulandira Baibulo limeneli sayenera kukakamizika kupereka ndalama yofanana ndi mtengo wake ngati sangakwanitse kutero. Aliyense angapereke ndalama zimene angathe.—2 Akor. 9:7.
◼ Ngati mukukonza zopita ku dziko lina limene silili pa lipoti latsopano la chaka chautumiki kapena dziko limene adiresi yake palibe patsamba lomaliza la buku latsopano la Yearbook, funsani ku ofesi yanu ya nthambi kuti akuthandizeni kudziwa zimene muyenera kusamala nazo kapena akupatseni malangizo apadera amene muyenera kutsatira. N’kutheka kuti ntchito ya Ufumu m’dzikolo ndi yoletsedwa. (Mat. 10:16) M’mayiko ena zingakhale zoletsedwa kuti alendo akumane ndi Mboni kapena mpingo wa m’deralo. Mungapatsidwenso malangizo ena okhudza ulaliki wa mwamwayi kapena zonyamula mabuku. Kutsatira malangizo amene mwapatsidwa kungakuthandizeni kupewa mavuto kapena kusokoneza ntchito ya Ufumu.−1 Akor. 14:33, 40.