Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira August 31, 2009. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya July 6 mpaka August 31, 2009. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 20.
1. N’chifukwa chiyani munthu anayenera kuphedwa ‘akatemberera’ makolo ake? (Lev. 20:9) [July 6, w04-CN 5/15 tsa. 24 ndime 6]
2. Popeza kuti Aisiraeli onse aamuna ankafunika kupita ku Madyerero a Mkate Wopanda Chotupitsa, ndani ankakolola barele woyamba kucha? (Lev. 23:5, 11) [July 13, w07-CN 7/15 tsa. 26 ndime 3]
3. Kodi Chaka Choliza Lipenga chimasonyeza zinthu zotani za m’tsogolo? (Lev. 25:10, 11) [July 20, w04-CN 7/15 mas. 26-27]
4. M’nthawi ya Isiraeli, kodi “chizindikiro” chotchulidwa pa Numeri 2:2 chinali ndi tanthauzo lililonse lokhudza kulambira? [July 27, w02-CN 9/15 tsa. 21 ndime 4]
5. Kodi olengeza Ufumu anthawi zonse masiku ano amasonyeza mtima wotani wofanana ndi umene Anaziri ankasonyeza m’nthawi ya Isiraeli? (Num. 6:3, 5, 6) [Aug. 3, w04-CN 8/1 mas. 24-25]
6. Kodi ndi mfundo iti ya lamulo la kupuma pantchito kwa a Levi yomwe ingagwire ntchito kwa atumiki a Yehova masiku ano? (Num. 8:25, 26) [Aug. 10, w04-CN 8/1 tsa. 25 ndime 1]
7. Kodi Aisiraeli anasonyeza bwanji “chilakolako,” kapena kuti mtima wadyera, ndipo zimenezi zikuwaphunzitsa chiyani Akhristu masiku ano? (Num. 11:4) [Aug. 17, w01-CN 6/15 mas. 14-15; w95-CN 3/1 tsa. 15 ndime 10]
8. N’chifukwa chiyani Miriamu yekha ndiye anakhala ndi khate, ndipo zimenezi zikutiphunzitsa chiyani? (Num. 12:9-11) [Aug. 17, w04-CN 8/1 tsa. 26 ndime 2; it-2 tsa. 415 ndime 1]
9. Kodi Yoswa ndi Kalebi anatanthauzanji pamene ananena kuti Akanani ndi “mkate”? (Num. 14:9) [Aug. 24, w06-CN 10/1 tsa. 16 ndime 5; it-1 mas. 363-364]
10. Kodi ndi chitsanzo chotichenjeza chotani chomwe chikupezeka pa Numeri 21:5? [Aug. 31, w99-CN 8/15 mas. 26-27]