Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu December: Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. January 2010: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? February: Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. Ndipo mu March: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
◼ Chikumbutso cha chaka cha 2011 chidzachitika Lamlungu, pa April 17, dzuwa litalowa. Taneneratu zimenezi kuti abale apezeretu malo ena ngati mipingo ingapo imagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi.
◼ Posachedwapa titumizira mpingo uliwonse timapepala toitanira anthu ku Chikumbutso ta m’chinenero chimene mpingowo umagwiritsa ntchito. Ngati m’gawo lanu muli anthu a zinenero zina ndipo mukufuna kuti tikutumizireni timapepala ta zinenero zimenezo, muyenera kuitanitsa timapepalato mwamsanga pa Fomu Yofunsira Mabuku (S-14) kapena pa adiresi ya pa Intaneti ya jw.org. Timapepalati tidzakhalapo m’Chichewa, m’Chingelezi ndi m’Chitumbuka.