Zimene Aliyense Angachite Pothandiza Ntchito Yolalikira Padziko Lonse
Baibulo linalosera kuti “idzafika nthawi yovuta yoikika,” ndipo linatchula kuti nthawi imeneyi ndi “masiku otsiriza.” (2 Tim. 3:1-5; 2 Pet. 3:3-7) M’nthawiyi, yomwe ndi inoyi, mavuto azachuma padziko lonse akuwonjezereka kwambiri. Choncho, ndi bwino kuganizira zimene tingachite pothandiza pantchito yolalikira yomwe ikuchitika padziko lonse ndiponso zimene tingachite kuti tipitirize kupereka ndalama zothandizira ntchitoyi.
◼ Mmene Gulu la Yehova Limapezera Ndalama: Gulu la Yehova si lolemera monga mmene anthu ena amanenera, koma ndi la anthu achikondi omwe siolemera. Komabe, iwo amaganizira anthu ena popereka chuma chawo ndiponso nthawi yawo moolowa manja. Nthawi zina zimakhala zovuta kuti tipeze ndalama zothandizira pantchito yosindikiza mabuku, zothandizira pamavuto adzidzidzi, pantchito yomanga Nyumba za Ufumu ndiponso kuthandizira pantchito zosiyanasiyana zomwe zikuchitika padziko lonse. Zimenezi zingafanane ndi zomwe zinachitika panthawi imene Nehemiya anayamba ntchito yomanganso mpanda wa Yerusalemu yomwenso inkaoneka yovuta. (Neh. 4:10) Komabe ntchitoyi inatheka chifukwa choti anaigawa kumabanja omwe anali ofunitsitsa kuigwira. Masiku anonso, kuti tipeze ndalama zokwanira kuthandizira pantchito ya padziko lonse, aliyense ayenera kuonetsetsa kuti akutenga nawo mbali mwa kupereka ndalama nthawi zonse.
◼ Zimene Munthu Aliyense Angachite Pothandiza Pantchito ya Ufumu: Popeza Yehova amadziwa bwino zolinga zathu komanso zimene tingathe kuchita, iye amayamikira tikamupatsa ndi mtima wonse, kaya ndi zambiri kapena zochepa. Pambali imeneyi, Yesu anasonyeza bwino kwambiri mmene Atate wake alili. Mwachitsanzo, kumbukirani mayi wina wamasiye amene anapereka ndalama zochepa. Baibulo limati: “[Yesu] atakweza maso anaona anthu olemera akuponya zopereka zawo moponyamo zopereka. Kenako anaona mkazi wina wamasiye wosauka akuponya timakobili tiwiri tating’ono mmenemo. Ndipo iye anati: ‘Kunena zoona, Mkazi wamasiyeyu, ngakhale kuti ndi wosauka, waponya zochuluka kuposa onse amene aponya. Pakuti onsewa aponya zopereka zimene atapa pa zochuluka zimene ali nazo. Koma mayiyu, mu umphawi wake, waponya zonse zimene akanatha kuchirikiza nazo moyo wake.’” (Luka 21:1-4) Yesu anaona kuti mphatso imene mkaziyo anapereka inali yamtengo wapatali chifukwa ankadziwa kuti anali wamasiye komanso wosauka, choncho anamuyamikira. Ndi mmenenso Yehova alili.—Yoh. 14:9.
Kodi masiku ano tingachite chiyani kuti tithandize pantchito yapadziko lonse? M’kalata yake yopita kwa Akorinto, mtumwi Paulo anatchula mfundo zitatu zokhudza kupereka ndalama mwa kufuna kwathu. (1) Ponena za kupereka ndalama, Paulo analangiza kuti: “Tsiku lililonse loyamba la mlungu, aliyense wa inu kunyumba kwake aike kenakake pambali.” (1 Akor. 16:2a) Choncho, tiyenera kukonzeratu zopereka zathu ndipo tizichita zimenezi nthawi zonse. Komanso munthu aliyense ayenera kupereka musadzionetsera ndiponso mwakufuna kwake. (2) Paulo analembanso kuti aliyense adzipereka “malinga ndi kupeza kwake.” (1 Akor. 16:22b, New International Version) Zimenezi zikutanthauza kuti munthu aliyense akafuna kupereka, adzipereka mogwirizana ndi ndalama zimene wapeza panthawiyo. Ngakhale atakhala wosauka kwambiri, Yehova amayamikira ndalama zochepa zimene munthuyo angapereke. (Luka 21:1-4) (3) Paulo analembanso kuti: “Aliyense achite mwa kutsimikiza kwa mtima wake, osati monyinyirika kapena mokakamizika ayi, pakuti Mulungu amakonda wopereka mokondwera.” (2 Akor. 9:7) Akhristu oona mtima amapereka ndi mtima wonse ndiponso mokondwera. N’zosangalatsa kuti ena ataona kuti amawononga ndalama zambiri poimba foni poyerekeza ndi zimene amapereka kumpingo, aona kuti ndi bwino kuchepetsa kuimba mafoni n’cholinga chakuti awonjezere ndalama zimene amapereka pothandiza ntchito ya Ufumu.
◼ Tiyesetse “Kuti Pasawonongeke Chilichonse”: Mfundo ina imene tiyenera kuitsatira ndi imene Yesu ananena pa Yohane 6:12. Ngakhale kuti iye anali ndi mphamvu zambiri zosandutsira mikate mozizwitsa, panthawi ina atamaliza kudya, anauza anthu kuti: “Sonkhanitsani zotsala zonse, kuti pasawonongeke chilichonse.” Kodi tingatani kuti titsatire mfundo imeneyi posamalira magazini ndi mabuku?
Popeza tikudziwa kuti mabuku athu ndi amtengo wapatali ndiponso kuti ntchito yofalitsa mabukuwa imafuna ndalama zambiri, kodi tingatani kuti tisamangopereka mabuku kwa anthu osayamikira? Njira imodzi ndiyo kufunsa munthuyo ngati akawerengedi buku kapena magazini amene mukum’patsa. Ofalitsa ena amazengereza kuuza anthu kuti ntchitoyi imathandizidwa ndi ndalama zimene anthu amapereka mwa kufuna kwawo. Koma nthawi zambiri ndi bwino kuwauza zimenezi chifukwa zimatithandiza kudziwa anthu amene ali ndi chidwi chenicheni. Tikamafotokozera anthu kuti ntchito yathuyi imafunikira ndalama, timasonyeza kuti timayamikira mabukuwo ndiponso timasonyeza kuti tikudziwa kuti papita ndalama zambiri kuti mabukuwa akonzedwe.
Komanso, akulu ayenera kuonanso kuchuluka kwa magazini amene mpingo umaitanitsa n’cholinga choti pasamakhale magazini ongounjikana m’Nyumba ya Ufumu.