Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu May: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mukamapanga maulendo obwereza kwa anthu achidwi, kuphatikizapo anthu amene anapezeka pa Chikumbutso kapena misonkhano ina koma sasonkhana nthawi zonse pamisonkhano ya mpingo, muyesetse kuyambitsa maphunziro a Baibulo pogwiritsa ntchito buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? June: Gawirani buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? July ndi August: Ofalitsa angathe kugawira lililonse la timabuku tamasamba 32 totsatirati timene mpingo uli nato. Dikirani!, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Mizimu ya Akufa Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, ndiponso Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!